Ofesi ya zaumoyo ku Zomba yayamba kupereka mankhwala a Likodzo

Advertisement

Ofesi ya zaumoyo Boma la Zomba yati yayamba kupereka mankhwala alikodzo komanso mankhwala a njoka zammimba kwa ana omwe ndi oyambira zaka zisanu (5) zakubwadwa kulekedza zaka khumi ndi zisanu zakubwadwa (15).

Wofalitsa nkhani ku ofesi yadza Umoyo Boma la Zomba Arnold Mndalira ndiyemwe wayankhula izi Lolemba pa nsonkhano wa atolankhani.

Mndalira wati ofesiyi ikuyembekedzereka kulandiritsa mankhwala a Alibendazole komanso a Praziquantel kwa ana osachepera 211,000 ndipo ntchitoyi ayigwira kwa masiku atatu omwe ndikuyambira pa 25 mpaka pa 27.

Iye wapempha mafumu kuti awuze makolo kuti alandiritse ana awo mankhwalawa kuti adziteteze kumatenda alikodzo komanso a njoka zam’mimba chifukwa matendewa ndi owopsa kwambiri.

Wofalitsa nkhaniyu wati office ya zaumoyo mu Boma la Zomba lasankha madera amafumu omwe kudagwa Namondwe wa Cyclone Freddy monga Namasalima, Likangala komanso Namitembo.

“Tilangize makolo kuti asaletse ana awo kulandira mankhwala amenewa chifukwa matenda a likodzo ndiwowopsa komanso tiwalangize kuti pamene akumwetsa ana mankhwala adzikhala atawapatsa chokudya chifukwa amapatsa njala,” adatero Arnold Mndalira.

Mndalira adati ogwira ntchito azaumoyo adziipereka mankhwalawa m’midzi yomwe yasankhidwa osati ku sukulu monga momwe amachitira ndi katemera wa polio.

Advertisement