Anthu a ku Dowa awonetsa chikondi pa mwana yemwe akupita ku Israel

Advertisement
People from Msakambewa at the Kamuzu International Airport

Anthu pamasamba a mchezo ayamikira anthu a kwa Msakambewa ku Dowa chifukwa cha chikondi chomwe awonetsa pa mwana wa m’mudzi mwawo yemwe akukapitiriza maphunziro ku Israel.

Anthu a kwa Msakambewa anatutana kupita ku bwalo lokwerera ndege la Kamuzu International kumuperekeza mwana wawoyi.

Malingana ndi kanema yemwe akuyendayenda m’masamba a mchezo, anthuwa anasonkha ndalama yomwe amupasa mnyamatayo kuti ayende nayo ndipo anaphika zakudya zomwe amadya ku bwaloli.

“Ndife a m’mudzi umodzi. Tonse tuperekeza mwana,” anatero anthuwo atafunsidwa ndi mayi yemwe amajambula kanemayo.

Boy from Msakambewa in Dowa
Ndikalimbikira: watero mnyamatayu

“Tikufuna ana a kwathu m’mudzi wathu apezepo phunziro,” anaonjezera m’modzi mwa amayiwo.

Mu mawu ake, mnyamatayo, yemwe anapanga digiri ku Luanar ndipo akukapanga Masters, wati anthuwo amulangiza kuti azikalimbikira sukulu.

“Akuti ndizilimbikira sukulu. Ine ndati eya ndizilimbikira,” anatero mnyamatayo.

Polankhulapo, anthu pamasamba a mchezo ati anthu a kwa Msakambewa aonetsa chikondi pa mnyamatayo.

“Zosangalatsa wapita nd madalitso mwanayu,” ena anatero.

Pomwe wina anati: Tinakamati tizikhara choncho kumalawi kuno bwezi kulibe ufiti chifukwa nsanje ndi sanamila imodzi yoyambitsa ufiti. Mulungu adalitse anthu a kwa Msakambewa chifukwa cha chikondi.”

Advertisement