Bambo wazaka 44 ali mchitokosi chifukwa chogwirilira anyamata


A man in Mchinji arrested for raping boys

Bambo wa zaka 44 amumanga ku Mchinji chifukwa chogwirilira anyamata awiri a zaka zosaposera 12.

Wofalitsa nkhani za apolisi ku Mchinji a Limbani Mpinganjira wati bamboyu dzina lake ndi James Makunganya.

Malingana ndi a Mpinganjira, bamboyu aampereka K500 kwa anyamatawa komanso amawaopseza kuti awapha akakawulula kwa makolo awo.

Koma anawa tsiku lina analimba mtima ndikuwawuza makolo awo za chipongwe chomwe a Makunganya amawachitira.

A Makunganya omwe amachokera m’mudzi wa Masautso mdera la mfumu yayikulu Zulu m’boma la Mchinji akuyembekezeka kukaonekela ku khoti kukayankha mlandu wogwirilira ana.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading