Mayi osamutsa katundu wa m’nyumba amugamula kukakhala ku ndende chaka chimodzi

Advertisement

Bwalo la milandu ku Dowa lagamula mayi wa zaka 42, Flora Thom, kukakhala ku ndende kwa chaka ndi miyezi itatu chifukwa chakuba katundu wa m’nyumba ya bwana wake wa ndalama pafupifupi K2 miliyoni.

Bwaloli linamva kuchokera kwa oyimira boma pamlanduwu, Sub Inspector Patrick Mandanda kuti pa 6 August 2023, a Thom anaba katunduyu pomwe abwana awo anapita ku tchalitchi.

Iwo adabwereka galimoto ya mtundu wa lorry ndikuba katunduyu koma anthu ena adawaona ndipo adayamba kuwamenya apolisi a Kanengo asanafike pamalopo.

Powonekera kubwaloli, iwo anavomera mlanduwu koma anapempha bwalo kuti liwakhululukire kaamba koti ali ndi udindo osamalira banja lawo komanso ndi koyamba kupalamula.

Koma oweruza mlandu Montfort Misunje anagamula kuti a Thom akhale ku ndende kwa chaka ndi miyezi itatu ndikugwira ntchito ya kalavula gaga.

A Thom amachokera mmudzi mwa Nangumi, mfumu yaikulu Chimaliro m’boma la Thyolo.

Advertisement