Boma la mgwirizano wa Tonse lati likubweza ngongole ya US$800 miliyoni yomwe linatenga boma la chipani cha DPP ndipo izi zikuchititsa kuti ndalama zakunja zizisowa m’dziko muno.
Wanena izi ndi nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu omwe amayankhula lero pa msonkhano wa olemba nkhani ku Lilongwe.
Msonkhanowu unapangidwa kuti boma lifotokoze bwino chifukwa chimene mafuta akusowela kuno ku Malawi.
Mu mawu awo, a Kunkuyu anati boma la DPP linatenga ngongole ku banki ya Afrixem ndipo ndalamazi zinkasungidwa ku banki yaikulu ya Reserve kuti zizionetsa ngati ndalama ya kwacha ili ndi mphamvu komanso ngati kuti dziko lino lili ndi ndalama zakunja.
Iwo anaonjezera kuti ndalamazi ntchito yake sinaoneke kwenikweni koma pano boma la Tonse layamba kuzibweza.
Malingana ndi a Kunkuyu, boma la Tonse motsogozedwa ndi a Lazarus Chakwera likumabweza ma dollar a ku Amerika okwana 100 milliyoni pa chaka.
A Kunkuyu ati izi ndi zomwe zikupangitsa kuti ndalama zakunja zisamapezeke komanso kuti mafuta azisowa m’dziko muno.
Ku msonkhano womwewo, a Kunkuyu anatinso boma la Tonse lakwanitsa kubwereka US$50 miliyoni zogulira mafuta.
Chaka chatha boma la a Chakwera linabwerekanso US$50 milliyoni yogulira mafuta