Anjatwa kaamba kogulira mafuta galimoto m’zigubu

Advertisement
Mafuta ku Malawi

Apolisi m’boma la Dowa a njata anthu khumi ndi m’modzi (11) kaamba kogulira mafuta a galimoto m’zigubu.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Dowa a Alice Sitima omwe afotokoza kuti anthuwa amangidwa kumathero asabatayi m’bomali.

A Sitima ati a polisi m’bomali anakhazikitsa chipikisheni m’madera ena m’bomali ndipo apa ndipamene anakumanizana ndi anthuwa omwe alandidwa mafuta a galimoto zomwe anagula.

Ofalitsa nkhaniwa ati apolisi alanda malita okwana makumi asanu ndi awiri (70) komaso ati alanda zigubu zopanda mafuta zokwana makumi atatu (30) zomwe ena mwana anthuwa amafuna kugwiritsa ntchito pogulira mafuta a galimotowa.

Izi zikudza pomwe posachedwapa apolisi mu mzinda wa Lilongwe analanda zigubu zoposera zana limodzi m’malo othilira mafuta agalimoto osiyanasiyana.

A polisi mu mzindawu anati anagwira ntchitoyi kaamba koti analandira ma lipoti oti anthu ochuluka akumagula mafuta agalimoto ndikumakawagulitsa mumisika ya m’makwalala pa mitengo yokwera kwambiri zomwe ati ndikuphwanya malamulo.

Ntchito yolanda zigubuyi ikutsatira chiletso chomwe bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) layika choletsa anthu kugula mafuta muzigubu makamaka pa nthawi ya nsautso wa mafuta a galimoto ngati ino.

Msabata yatha, akuluakulu a chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe adandaula ndikuchuluka kwa anthu omwe chipatalachi chikulandira omwe ati akumakhala akakhudzidwa ndi ngozi ya moto oyamba chifukwa cha mafuta a galimoto.

Akuluakulu a chipatalachi alangiza anthu m’dziko muno kuti asiye nchitidwe osunga mafuta a galimoto m’nyumba zawo ponena kuti ndi omwe ukukolezera ngozi za moto zomwe pamapeto pake zikupha anthu ochuluka.

Pakadali pano anthu akumachita kugonera m’malo omwetsera mafuta a galimoto kuti agule malondawa zomwe zapangitsa kuti ntchito za ntengatenga ndi ntokoma zikhale pa chipsinjo.

Advertisement