Mkaidi wathawa ku ndende ya Zomba

Advertisement

Akulu akulu a ndende ya Zomba atsimikiza kuti mkaidi m’modzi wa zaka 33 wathawa pomwe amagwira ntchito lero Lachiwiri.

Malinga ndi m’modzi mwa akuluakulu a ndendeyi a  Harrings Nyalubwe wazindikira mkaidi othawayu ngati Jimu Jabu.

A Nyalubwe awuza nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno kuti Jabu wathawa m’mawa wa Lachiwiri pa 21 May 2024 pomwe amagwira ntchito zina ngati mbali imodzi ya chilango chawo.

Iwo ati Jabu anali m’gulu la a kaidi  ena omwe amagwira ntchito pa munda wina wa Nandolo ku m’mawaku ndipo kenaka anazemba mkati mwa ntchito mkuthawa.

A Nyalubwe ati patapita ka nthawi pang’ono, akuluakulu a ndende omwe amayang’anira akaidiwa, anadabwa kuti chiwerengero chimachepelako ndipo apa ndi momwe zinadziwika kuti Jabu wathawa.

Pakadali pano akuluakulu andendeyi akhazikitsa ntchito yosaka mkaidiyo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.