DStv ikhale, ipite? Wakula mtsutso

Advertisement
Multichoice Malawi

…ena akuti MACRA ipepese kwa MultiChoice, ichotse chiletso

Njovu zikamamenyana: Pamene ena akukondwera ndi ganizo la MultiChoice Africa lochotsa ma sevisi a DStv mdziko muno, ena akukhetsa misozi komanso tikukamba pano chimtsutso chandiwe yani chabuka m’masamba anchezo; nanga inu muli mbali iti, DSTV ikhale kapena itsetseleke?

Kampani ya Multichoice Africa Holdings (MAH) lachiwiri inadzidzimutsa a Malawi ochuluka ndi nkhani yoti ikuchotsa ma sevisi (service) a DStv kaamba kolephera kumvana chichewa ndi akuluakulu a bungwe la MACRA pankhani yokweza mitengo.

Bungwe la MACRA linatenga chiletso choletsa kampani ya MAH kukweza mitengo yomwe anthu amalipira akafuna kuonera ma pakeji (package) osiyanasiyana pa DStv zomwe zakwiyitsa kampaniyi.

Podziwa kuti nkhonya yobwezera kuwawa, kampani ya MAH yalengeza kuti kuyambira pano, ma sevisi a DStv sapezekaso mdziko muno ndipo yati kuyambira pa 9 August, 2023 ma kasitomala a DStv sangatheso kulipira kuti DStv yawo isaduke.

Nkhaniyi yadzetsa mtsutso wandiweyani pakati pa anthu mdziko muno makamaka m’masamba a nchezo pomwe a Malawi ochuluka akupeleka maganizo osiyanasiyana za ganizo la Multichoice Africa.

Poyankhula za nkhaniyi pa tsamba la fesibuku, munthu wina wati bungwe la MACRA likuyenera lichotse chiletso chomwe linatenga komaso lipepese ku kampani ya MAH ndicholinga choti ma sevisi a DStv asachotsedwe mdziko muno.

“Tisaayiwale kuti ku Malawi boma sililowelera ku ntchito za amalonda ndipo palibe amakakamizidwa kulipira Dstv. Zimatengela mthumba mwa munthu.

“Komanso Dstv simaletsa ma kampani ena kubwera ku Malawi ndiye ngati a MACRA akuona kuti kuli ena opereka ma sevisi abwino awapatse chilolezo abwere. Kwacha inagwa ndiye sizoona kuti tiziyembekeza kuti mitengo ya DStv ikhale chomwecho,” atero a Suleman.

Munthu winaso pa tsamba la thwita (twitter) wati ndiodandaula ndi nkhaniyi koma naye waloza chala bungwe la MACRA ponena kuti chiletso chomwe linatenga choletsa MAH kukweza mitengo ya DStv chinali chosayenera.

“Apapa sizinayende bwino. Multichoice Africa siyimakakamiza anthu kuonera DStv. Njira yabwino inali kukambirana kuti mtengo wawo usakwere kwambiri, osati mpaka kupita ku khothi nkhani lake izizi, apapa nde atipweteka kwambiri kunena zoona. Koma ngati nkotheka kambiranani, DStv isachoke. Mpira tiwonera kuti?” wadandaula munthu wina pa thwita.

Mbali inayi, ena akuti palibe nkhani yodandaulitsa pa ganizo la Multichoice Africa Holdings kaamba koti a Malawi ambiri samawonera kale DStv chifukwa ndiyolowa mthumba kwambiri kuyelekeza ndi ma TV ena.

“Enanu ndikukudabwani kuti mukudandaula chiyani ngati kwanu kuli DStv. Tiyeni tiyang’ane chitsogolo basi, izi zomangoliralira zitichedwetsa. Bravo MACRA, mwagwira ntchito kwabasi, anthu awa asamatijaile,” watelo mkulu wina pa fesibuku.

Katswiri pa nkhani ya zipangizo zamakono yemweso ndi mkulu owona za makina osiyanasiyana ku kampani ya Ashley Media a Henry Kapitapita, ati ganizo la MAH litsekule m’maso atsogoleri a dziko lino pa nkhani ya ziphaniphani.

A Kapitapita ati izi zikusonyezeratu kuti dziko lino likuyenera kukhala ndi ma kampani ake ake ofanana ndi kampani ya MultiChoice zomwe akuti zitha kuthandiza kuti mavuto a mtundu ngati uwu athetsedwe m’dziko muno.

Pakadali pano, bungwe last MACRA silinayankhule kali kose zokhudza ganizo la Multichoice Africa Holdings lochotsa ma sevisi a DStv m’dziko muno.

Advertisement