Pamene dziko lino likuvutika pa nkhani ya zachuma, phungu wa nyumba ya malamulo wa dera la kum’mwera kwa boma la Chitipa a Werani Chilenga, ati akufuna kuti nyumba ya malamulo ikambirane zoti aphungu opuma azilandira malipiro a pamwezi kwa moyo wawo onse.
Izi ndi malingana ndi chikalata cha a Chilenga chomwe chikuzungulira m’masamba a mchezo chomwe chikusonyeza kuti iwo akulingalira zopititsa nkhaniyi ku nyumba ya malamulo kuti aphungu akakambirane za nkhaniyi.
A Chilenga ati akuganiza zopititsa nkhaniyi ku nyumba ya malamulo kaamba koti akuona kuti aphungu opuma ambiri akuvutika m’makwalalamu chifukwa choti samalabadilidwa pamene agwa pa zisankho kapena apuma mwakufuna kwawo.
Iwo ati izi sizabwino potengera kuti anthuwa amatenga nawo gawo lalikulu pa ntchito yotukula dziko lino ndipo ati nkoyenera kuti azilandira ndalama pamwezi uli onse kwa moyo wawo onse ngati njira imodzi yowathokozera.
Phunguyu wati atha kukhala okondwa kwambiri ngati aphungu opuma onse mdziko muno azilandira theka la ndalama zomwe aphungu apano akulandira pakutha pa mwezi uli onse kufikira atatsamira mkono.
Ngati pempho la a Chilenga litavomelezedwa, zikutanthauza kuti aphungu opumawa atha kumalandira ndalama zosachepera K2,000,000 mwezi uliwonse kwa moyo wawo onse.
Pakadali pano, anthu ambiri omwe akuyankhula za nkhaniyi makamaka m’masamba a mchezo, ati uku ndikuganiza mobwelera m’mbuyo ndipo ena akuti ganizo la a Chilenga silingapindulire dziko lino.
“Za mkutu za ziii. We don’t have such money (tilibe ndalama zimenezo). Aphungu ndalama zimathera azimai. Madyo,” watelo Joshua Chisa Mbele patsamba lake la fesibuku.