A Yesu amakukhala’; Shammah Vocalz watenga tchuthi kuimba zauzimu

Advertisement

M’modzi mwa anamandwa poyimba nyimbo zauzimu Shammah Sitola yemwe amadziwika kuti Shammah Vocalz walengeza kuti watenga kaye tchuthi kuimba nyimbo zauzimu.

Oyimbayu waulura za nkhaniyi lero lolemba pa 26 June, 2023 kudzera patsamba lake la fesibuku.

Shammah yemwe anaimba nyimbo yotchuka ya ‘Zoe’, wati chiganizochi chabwera kaamba koti akudziona kupelewera pa uzimu ndipo wati sangakhale akuyimbira Yehova akudzimva choncho.

Iye waonjezera kuti azayambiraso kuimba nyimbo zauzimu pokhapokha adzaone kuti uzimu wake wafika pomwe akufuna.

“Ndikuona ngati sindine oyenera kukhala oyimba nyimbo za uzimu, choncho kufikira nthawi imeneyo, sindizitakataka. Zikomo,” watelo Shammah mu utgenga wake.

Nkhaniyi yalandilidwa mosiyanasiyana kaamba koti ena akuti ichi ndichaganizo cholakwika pomwe ena akuti ichi ndichoganizo chabwino ponena kuti oyimba nyimbo zauzimu samapeza phindu kwenikweni kuyelekeza ndi oyimba nyimbo wamba.

“Mmmmh bwanji shamma, ineyo I see u kut sunakopeke ndi za m’dziko,enawa timadziwa kuti ku gospel angobisalirako koma amapanga ntchito zakumidima, my brother be strong kukhala opemphera munthu umakumana ndi ma temptations ambiri koma ukadziwa chimene uli sumatekeseka, we Love u en ur music,” wadandaula munthu wina.

Mmodzi mwa oyimba nyimbo zauzimu, Stevie Wazisomo Muliya wamulimbikitsa mzakeyu kuti anthu tonse timakhala mwa chisomo cha Mulungu.

“Sala (sir), tonse timakhala mwa chisomo cha Mulungu molingana ndi malembo opatulika. 2 Akorinto 5:21 baibulo limati Kristu anapangidwa wauchimo kuti mwa Iye tikhale olungama mwa Mulungu,” watelo Muliya.

Oyimbayu anadziwika bwino bwino pa nkhani za maimbidwe mchaka cha 2011 ndipo zina mwa nyimbo zake zotchuka ndi monga; ‘No reverse’, Shibobo’, ‘Daily’ komaso ‘No stress’.

Advertisement