A Thomas Damiyano a m’mudzi mwa Kazembe Mfumu yaikulu Kachindamoto M’boma la Dedza ati chiwapezereni ndi nthenda ya Khate chaka chatha moyo wawo sunasinthe kwenikweni chifukwa akukwanitsabe kugwira ntchito zomwe zimawapezetsa ndalama pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku koma adandaula kuti amasalidwa ndi anzawo ena.
Makolo ake a Thomas komanso abale ake awiri nawonso anapezeka ndi nthendayi ndipo pano akumwa mankhwala omwe analandira kuchiptala.
Thomas wati iyeyu amangomva kupweteka m’miyendo pa nthawi yomwe akufuna kugona usiku koma tsiku lonse amagwira ntchito zake bwinobwino.
“Pankhani yakusalidwa tisamasalidwadi, anzanga ena amakana kucheza nane pamene ena timacheza bwinobwino zomwe zimakhala zokhumudwitsa banja lonse.
“Ndikupempha akufuna kwabwino kuti atithandize zinthu ngati zakudya komanso ndalama yomwe ndingathe kuyambira bizinesi,” Thomas anatero
Stella Damiyano yemwe naye anapezeka ndi nthendayi wati akumva ululu komanso pano akukanika kugwira ntchito mwayekha.
Mkulu Owona matenda apakhungu ku Mchinji a Odala Mbewe ati nthenda yakhate imatenga nthawi kuti munthu azindikire kuti akudwala nthendayi koma ngakhale zili chomwechi munthu akamamwa mankhwala mwa ndondomeko amachira.
A Mbewe anati ena mwa anthu amene apezeka ndi nthendayi anasiya kumwa mankhwala ataona kuti ayamba kuchira chinthu chomwe chimankhala chodandaulitsa chifukwa amakhala kuti akuyenera kupitiliza kumwa mankhwala anthendayi.
“Kota ya chaka cha 2022 chiwerengero cha anthu odwala nthenda ya Khate anali 64 mwa anthu amenewa 43 anali abambo ndipo 23 anali amayi komanso tinalandira anthu awiri omwe anali atsopano.
“Kota ya Chaka chino talandira chiwerengero chokwana 79 ndipo pa anthu amenewa abambo alipo 46 ndipo amayi alipo 31 ndi chiwerengero cha anthu 6 Cha sopano”, adaonjezerapo a Mbewe.
Ambewe ati anthu tsopano akudzindikira za nthendayi pang’onopang’ono chinthu chomwe ndi chodalitsa chifukwa akumapezeka athamangira ku chipatala nsanga.
Follow us on Twitter: