…watsindika zakufunika kwa ulamuliro wa mzigawo
Mtsogoleri wa chipani cha Alliance for Democracy (AFORD) Enoch Chihana wati chipani chawo sichilowaso mu mgwirizano ndi zipani zina pa chisankho chikubwerachi ponena kuti akuona kuti nthawi yoti AFORD ilowe m’boma yakwana.
A Chihana anayankhula izi Lolemba pa msonkhano omwe chipanichi chinachititsa ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre komweso chipanichi chimakondwelera kuti chakwanitsa za makumi atatu (30) chikhazikitsidwileni.
Iwo anati potengera kuti chipanichi chakhalitsa m’dziko muno, saloraso kukhala m’nkhwapa mwa zipani zina ponena kuti akuona kuti nthawi yakwana kuti chipani cha Aford chilamulire dziko lino.
“Ine ndi anzanga tili pano sitingavomeleze kuti ife ngati chipani cha AFORD tikhale m’nkhwapa mwa inu, ayi. Tisiyeni ndife chipani pachokha, lnuso ndinu chipani panokha, aliyese ndi pulezidenti payekha ineso ndine pulezidenti pandekha ku chipani changa Aford, tisiyeni.
“Patsogolo ife a Afford tikuti nthawi yaife osati yanu yakwana, nafeso tilowe m’boma. Mufune kapena musafune, mukondwe kapena musakondwe koma Aford 2025 tiyima tokha,” atelo a Chihana.
Iwo adandaula kuti iwo pamodzi ndi a Joyce Banda anaponyedwa miyala ngakhale kuti anali amodzi mwa anthu omwe anathandizira kuti m’gwirizano wa Tonse utenge boma pa chisankho cha mu 2020.
A Chihana anatsindika kuti zipani za Malawi Congress (MCP), United Transformation Movement (UTM), sizinakakwanitsa kusowa m’boma popanda kukhazikitsidwa kwa mgwirizano wa Tonse.
“MCP payokha sikanawina boma, UTM payokha sikanawina boma, Aford payokha sikanawina boma. Tinapangana kuyenda ulendo ndikutsogoza munthu mmodzi amene akhale pulezidenti. A Chakwera patsogolo Saulos pambuyo, ife tijiyile ma minibasi adzadze. Koma pamapeto pake basi itadzadza inanyamuka koma ine ojiyilira pamodzi ndi mayi Joyce Banda adatisiya pa Chinsewu padepoti,” anadandaula choncho a Chihana.
Mkuluyu wanenetsa kuti a Malawi ayiwale kukwanilitsidwa kwa malonjezo omwe akuluakulu a mgwirizano wa Tonse ankalonjeza nthawi yokopa anthu zomwe ndikuphatikiza feteleza otsika mtengo.
“Hisitole (history) ya Tonse alayansi ndiyoti siyingakupatseni feteleza, siyikupatsani chakudya, siyikupatsani zintchito, zimenezo ndi hisitole, tiyeni tiyang’ane patsogolo,” anawonjezera choncho a Chihana.
Pakayandetsedwe ka dziko, a Chihana anati dziko lino liyende bwino, pakuyenera pakhazikitsidwe ulamuliro wa mzigawo omwe akuti utha kuthandiza kuti chitukuko chifikire zigawo zonse mdziko muno.
Apa iwo apempha mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti akasiye nkhaniyi ku bungwe lowunika za malamulo la Malawi Law Commission komaso kuti ayitanitse lifelendamu (referendum).
“Nkhani ya ma boma a mzigawo muyitengere ku bungwe la Law Commission kuti akawunikire kuti kuno ku Malawi boma limeneli litha kukhala la mtundu wanji. Chachiwiri muyitanitse constitution conference yomwe tiyitane akatswiri ochokera m’maiko momwe muli boma la mzigawo. Ndipo chomaliza muyitanitse lifelendamu, anthu akepeleke maganizo awo,” anateloso a Chihana.
Chipani cha Aford chinakhazikitsidwa m’chaka cha 1993 motsogozedwa ndi mtsogoleri wake oyamba malemu Chakufwa Chihana ndipo ndi chimodzi mwa zipani zomwe zinalimbikitsa kuti m’dziko muno mukhala ulamuliro wa zipani zambiri.