Gulu la anthu ena omwe akuzitchula kuti nzika zokhudzidwa, zati sizoyenera kuti dziko lino liziloleza maukwati amuna kapena akazi okhaokha.
Poyankhula ndi tsamba lino, mmodzi mwa mzika zokhudzidwazi a Edward Kambanje omwe ndi wa chiwiri kwa wapampando wa gululi, ati mchitidwe wa mathanyula ndi mwikho ku dziko lino.
A Kambanje anati dziko lili lonse limakhala ndi chikhalidwe komaso mbiri yomwe akuti imakhala yosiyana ndi dziko lili lonse choncho mchitidwe ogonana amuna kapena akazi okhaokha, ikutsutsana ndi chikhalidwe cha dziko lino.
“Mchitidwe wa mathanyula ukutsutsana ndi chikhalidwe cha dziko lathu. Choncho ife ngati mzika zokhudzidwa tikukanitsitsa mwantu wa galu mathanyula, sitikuwafuna kuno ku Malawi.
“Dziko la Malawi limadziwika kuti ndi dziko lowopa Mulungu, nde mukufuna mundiuza kuti Mulungu angasangalale kuti dziko lathu liloleze maukwati amuna kapena akazi okhaokha? Yankho ndi ayi, ndiye ndi chifukwa chake ife tikuti mathanyula kuno ayi,” watelo Kambanje.
Mkuluyu wati gulu lawoli lachitatu lino likhala likuchititsa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre komwe akuyenera kukafotokoza tchutchu zomwe gululi likudana nazo pankhani ya maukwati amuna kapena akazi okhaokha.
A Kambanje awonjezera kuti pa msonkhano wa atolankhaniwu akufuna akameme boma, mabwalo a milandu komaso atsogoleri a chipembedzo kuti asalole kuti dziko lino livomeleze ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha.
“Ndizoonadi tili ndi msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre. Kumeneku tikakhala tikufotokoza tchutchutchu zifukwa zomwe tikunenera kuti dziko lino lisaloleze mchitidwe wa mathanyula,” anaonjezera choncho a Kambanje.
Ena mwa anthu omwe ali mgulu la mzika zokhudzidwazi ndi a Victor Nyanyaliwa omwe ndi wapampando wagululi komaso a Oliver Nakoma omwe ndi membala.
Nkhaniyi ikudza kutsatira kukhazikitsidwa kwa bwalo la milandu pa zamalamulo lomwe pa 23 mwezi uno likuyenera liyambe kumva pempho loti dziko lino liyambe kuloleza ma ukwati amuna kapena akazi okhaokha.
Follow us on Twitter: