CCAP yapepesa alhomwe, akhilisitu ake ponyazitsidwa ndi abusa awiri

Advertisement

Akuluakulu a Sinodi kulankhula ndi atolankani

Sinodi ya Blantyre mu mpingo wa CCAP, yapepesa kwa anthu amtundu wachi lhomwe komanso a khilisitu ake kaamba kosambulidwa ndi abusa awiri omwe sakumwerana madzi atasemphana chichewa.

Mkati mwa sabatayi, tsamba lino linaulutsa nkhani yoti abusa awiri a sinodiyi apindirana ndevu mkamwa potsatira chisankho cha adindo chomwe sinodiyi ikuyembekezeka kuchititsa chaka chino.

Malingana ndi kilipi (audio clip) yomwe anthu akugawanabe m’masamba a mchezo, m’busa wina akuloza chala m’busa nzake kuti akumachita ugogodi ndicholinga choti a Billy Gama adzawinenso pa udindo wa ulembi wa sinodiyi pa zisankhozo.

M’busa wokwiyayu adawopseza kuti alowa pa galaundi ndipo anzakwo sangamugwedeze kumbali yolodzana muufiti komaso kumbali ya zigogodo.

Kupatula apo, m’busayu ananyozaso anthu amtundu wa chilhomwe kuti ndi chulu cha ndiwo, zomwe zinakwiyitsa anthu amtunduwu ponena kuti iwo kukhala munthu wa Mulungu sanayenera kufika pamlingo umenewo.

“Achimwene ineyo ndikhoza kukumenyani pamanja komaso olo paufiti ndikhoza kukumenyani.

“Ngati ili ndewu nditha kubwera pakhomo panu mawa kuti ndimenyane nanu. Ineyo ndatopa, ndatopa nanu alomwe zitsilu zachabechabe,” anatero m’busa okwiyayo.

Potsatira nkhaniyi, akuluakulu a sinodiyi abwera poyera ndikupepesa ku mtundu wa aMalawi makamaka kwa anthu amtundu wa chilhomwe komaso akhilisitu ampingowu kaamba ka zomwe zachitikazi.

Mlembi opuma wa sinodi ya Blantyre, m’busa Silas Ncozana yemwe amayankhula m’malo mwa komiti yapadela yomwe sinodiyi yakhazikitsa kuti ikambilane zankhaniyi, wauza imodzi mwa nyumba zowulutsira mawu mdziko muno nkhaniyi ndiyochititsa manyazi.

Ncozana wati mawu omwe anagwilitsidwa ntchito ndi abusawa anali osavomelezeka komanso osayenela kuchoka pakamwa pa mtumiki wa Mulungu ndipo apempha chikhululukilo kwa anthu omwe akhudzidwa ndi nkhaniyi.

Iwo anaonjezera kuti akudziwa kuti zomwe zinachitikazi zinakhumudwitsa akhilisitu ampingo wawo komanso anthu ena, ndipo ati pakadali pano akupanga dongosolo loyitanitsa abusa awiriwa kuti athetse kusavetsetsanaku.

Follow us on Twitter:

Advertisement