Muli uthenga mu kugonana. Ndi chinthu chokongola kwambiri – watero Papa

Advertisement

…Wadzudzula mchitidwe ozithandiza wekha

Kudya beti ndi kosangalatsa inde. Kwa ena kupambana mayeso kumene kutha kukhala chinthu cha mtengo wa pamwamba. Koma zonsezi sizingafike pa kugonana. Kugonana ndicho chinthu chokongola kwambiri pa dziko pano, watero mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse, Papa.

Malinga ndi pologalamu ya padera imene ikupezeka pa Disney +, mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu anauza anthu amene amafunsa mafunso kuti kugonana ndi chinthu chopambana ndinso chokongola kwambiri.

“Kugonana ndi chinthu cha mtengo wa patali chimene Mulungu anapatsa munthu,” anatero Papa.

Iye anaonjezera kuti mu kugonana muli chidzalo ndipo anadzudzula zinthu zonse zimene zimasokoneza anthu kupeza uthenga mu kugonana.

Iye ananena kuti mchitidwe ozithandiza wekha munthu chilakolako chikakupeza ndi wa chabe chifukwa umasokonezana ndi uthenga umene uli mu kugonana.

“Munthu kutha kusangalatsa wina, iwenso ndi kusangalala kudzera mu njira yogonana ndi chinthu cha mtengo wa patali,” anatero podzudzula anthu okonda kuzithandiza okha.

Advertisement