Anthu ochuluka m’dziko muno akupitilira kukanitsitsa mwantuu wagalu lamulo lomwe walamura posachedwapa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti nyimbo ya fuko iziyimbidwa ndime zonse zitatu.
Lachisanu lapitali a Chakwera analamura kuti nthawi zonse pa malo aliwonse amene nyimboyi idziyimbidwa, anthu adziyimba ndime zonse zitatu osangoti ndime imodzi monga momwe anthu akhala akupangira kumbuyo konseku.
A Chakwera omwe amayankhula izi mumzinda wa Lilongwe pa mwambo olimbikitsa umodzi ndi mtendere mdziko muno, anati ndime ziwiri zomwe siziyimbidwazo zimalimbikitsa umodzi wa anthu mdziko muno choncho mkofunika kuti zidziyimbidwaso.
Kulamulaku sikunasangalatse a Malawi ochuluka ndipo anthu ochuluka omwe akuyankhula za nkhaniyi makamaka mmasamba anchezo, ati sakuona phindu lomwe anthu mdziko muno angapeze pakuimba nyimbo yafukoyi ndime zonse zitatu.
Anthu ena pa fesibuku komaso thwita ati a Chakwera akuyenera kukhala kalikiliki kusaka njira zothetsera mavuto adzawoneni omwe anthu mdziko muno akukumana nawo osati kulamura zinthu zomwe zilibe phindu kwenikweni.
A Alick Kazembe omwe anathilira ndemanga pa tsamba lathu la fesibuku pankhani yokhudza zomwe a Chakwera analamulazi, anati; “Anthu akungomwa madzi mphamvu zoimbira nyimbo yonse zichokela kuti bwana?”
Nawo a Petros Banda anati; “Mr president ndibwino akadangokwanisa zomwe analonjeza kwa amalawi, osati kuwauza aMalawi kupanga zimene sanalonjeze zoimba nyimbo.”
Ndipo nawo a Busyb Khang’a anaonjezera ndikunena kuti; “Kodi dzikoli liri mmavuto chifukwa choti nyimbo ya fuko la Malawi imayimbidwa ndime imodzi yokha basi?”
Mbali inayi a Sammy Examine Enginez sanafune kupsatira mawu koma kufunsa ngati izi zili ndikuthekera kuthetsa mavuto mdziko muno.
“Ngat izi zingathese ziphuphu, kubweletsa forex, kupezeka kwa mafuta, kutsika kwa mitengo yazinthu then a Malawi azitelo. Unless the people have a chicken Brain they can sing all verses (ngati anthu ali ndiubongo wa nkhuku adziimbadi mavesi onse)”
Anthu ena ati lamulori litha kutenga nthawi yayitali kuti likwanilitsidwe ati kaamba koti sizophweka kuti anthu aloweze mavesi awiri omwe amatsalirawo.
Ndime zonse zitatu za nyimboyi ndi izi:
“Mlungu dalitsani Malaŵi,
Mumsunge m’mtendere.
Gonjetsani adani onse,
Njala, nthenda, nsanje.
Lunzitsani mitima yathu,
Kuti tisaope.
Mdalitse Mtsogoleri nafe,
Ndi Mayi Malaŵi.
II
Malaŵi ndziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi mphepo ya m’mapiri,
Ndithudi tadala.
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
N’mphatso zaulere.
Nkhalango, madambo abwino.
Ngwokoma Malaŵi.
III
O Ufulu tigwirizane,
Kukweza Malaŵi.
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire.
Pa nkhondo nkana pa mtendere,
Cholinga n’chimodzi.
Mayi, bambo, tidzipereke,
Pokweza Malaŵi.”
Follow us on Twitter: