A unduna wa zamalimidwe atsutsa maripoti oti akathyali ena anawachenjeretsa ndalama zokwana 30 billion za fetereza otchipa. Malinga ndi maripoti amene atchuka, ati ma dobadoba ena a ku United Kingdom anatsekula mmaso boma la a Chakwera polidyera 30 billion ya ndondomeko ya AIP.
Maripotiwa ati kampani ina ya dziko la UK inalonjeza kubweretsa fetereza ku Malawi pa mtengo osaboola mthumba. Ati a boma atamva izi, analowa mu mgwirizano ndi kampani iyi kuti iwapatse fetereza. Mwa mgwirizano, kampani inanena kuti ikufuna dipoziti ya 30 billion ndipo inapatsidwa.
Malinga ndi phungu wa kunyumba ya malamulo a Sameer Suleman amene amatsogolera komiti yoona za ulimi mu nyumbayi, zikuoneka kuti kampani iyi italandira ndalamazo inasowa nazo basi ndi kuchita u dobadoba.
Izi zapangitsa kuti a Malawi ena anene kuti ndalama za boma anadyetsa ku njuga, ati ku masewero a chi Aviator.
Koma polankhulapo pa nkhaniyi, a unduna wa zamalimidwe ati ndi zabodza zoti misonkho ya a Malawi yokwana 30 billion inadyedwa ndi anyamata a patauni. Iwo apenekera kuti ngati kungakhale kuchenjeretsedwa, ndiye anaberedwa 725 million Kwacha basi.
“Si zoona za 30 billion. Chilungamo ndi choti ife tinachita mgwirizano ndi kampani ina ku Mangalande yomwe inalonjeza kutigulitsa fetereza. Tinapereka 725 million yoyambira. Kenako kampani idanena kuti yalephera kukwanitsa,” atelo a undunawu.
Iwo ati pano akudikira kuti kampani iyi ibweze ndalamayo.