Tikudutsa muzowawa: Escom yapempha kukwezedwa mtengo kwa magetsi


Pamene anthu m’dziko muno akupitilira kudandaula za zikhomo pankhani ya zachuma, kampani yogulitsa magetsi ya Electricity Supply Corporation of Malawi (ESCOM) yati ikufuna mtengo wa magetsi ukwere apo bii kampaniyi itsekedwe kaye.

Izi ndi malingana ndi mkulu wakampaniyi a Kamkwamba Kumwenda omwe amayankhula lachiwiri pamsonkhano wa atolankhani omwe unachitikira kumaofesi akampaniyi mumzinda wa Blantyre.

A Kumwenda awuza atolankhani pamsonkhanowu kuti kuyambira pomwe kampaniyi inagawidwa mumchaka cha 2018, ikukumana ndizokhoma ndipo yati siikupanga phindu lili lonse pa ntchito yake yogulitsa magetsi.

Iwo anati mwachitsanzo, kuchoka mchaka cha 2018 kufika pano, kampaniyi yalephera kupanga phindu pa ntchito yake ndipo ati mmalo mwake, kampaniyi yaluza ndalama zokwana K112 biliyoni.

Iwo anati zonsezi ndikamba koti kampani ya ESCOM imagula magetsi ku kampani yopanga magetsi ya Egenco pa mtengo otsika wa K140 pa unit ndipo iyo imagulitsa kwa makasitomala ake pa mtengo wa K104 pa unit.

Iwo apempha kuti pakufunika mtengo wa magetsi ukwezedwe ndipo ati ngati izi zingalepheleke, kampaniyi ikuyenera kutsekedwa.

“Pang’ono ndi pang’ono ESCOM ikufa. Tikuyenera tiyitseke kapena tikweze mtengo wa magetsi. Choncho tikupempha kuti mtengo wa magetsi ukwezedwe. Pakadali pano tikukanbilanabe ndi bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) zankhaniyi,” atelo a Kumwenda.

Pakadali pano, mphekesera zikuveka kuti bungwe la MERA likuwunika mitengo yomwe bungwe la Escom likupempha kuti likweze.

One comment on “Tikudutsa muzowawa: Escom yapempha kukwezedwa mtengo kwa magetsi

  1. Ngat bungwe malingana ndi kafukufuku wanu zikhoza kukhala zoona kuti palidi Mavuto omwe mukukumana nawo,monga Ena mwatchula kale, komanso mongotengela ndi zofunikila pa umoyo wa anthu panopo zinthu sizili bwinonso,katundu wambili ofunikila wakwela kale mitengo kangapo konse koma anthufe kupeza kwathu ndkovutanso,ndikomwekaja,

    Zingoutsa nkwiyo wa anthu!
    Boma lilowelelepo pamnepo.

Comments are closed.

Discover more from Malawi 24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading