M’malawi ndi ena atatu akunja amangidwa ku South Africa

Advertisement
Malawi24

Apolisi m’dziko la South Africa amanga nzika ya dziko la Malawi ndi anthu ena atatu akunja powaganizira kuti anaba ma galimoto awiri a mtundu wa Toyota Fortuner ndi Mercedes Benz zomwenso amafuna azizembetse kutuluka nazo m’dzikolo.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za a Polisi ya m’boma la Limpopo, Brigadier Hlulani Mashaba, anthu atatuwa amangidwa kumathelo a sabata yatha pomwe anthu ena anatsina khutu a Polisi m’dzikolo za nkhaniyi.

Brigadier Mashaba wawuza nyumba zowulutsa mawu m’dzikomo kuti akathyaliwa amafuna kuzembetsa magalimotowa pobweretsa imodzi kuno ku Malawi ndi ina ku Zimbabwe.

A Mashaba ati a Polisi m’dzikolo atatsinidwa khutu za nkhaniyi, anakhazikitsa kafukufuku yemwe wapangitsa kuti anthu anayiwa, omwe mayina awo sanadziwike, kuti amangidwe. 

Wofalitsa nkhani za Polisiyu wati Lamulungu pa 28 April, 2024, cha m’ma 9:30 usiku, anagwira mzika ya ku Malawi-yi yomwe imayendetsa galimoto yotuwa ya Toyota Fortuner 2.8 mu msewu wa R101 omwe umalunjika ku Polokwane.

A Polisiwa akuti anadabwa kuti pomwe anaimitsa galimotoyi, shoveliyu sanayime ndipo m’malo mwake adayithamangitsa kwambiri kuthawa zomwe zinatsimikizira a chitetezowo kuti mphekesera zomwe anauzidwazo zinali zowona. 

Apa a Polisiwo nawo analikumba liwiri la mtondo wadooka pa galimoto zawo kuthamangitsa galimotoyo mpaka pomwe idayimitsidwa pafupi ndi Polokwane Shell Ultra City kudera la Polisi la Westenburg.

A polisi ati anthu anayiwa akuyembekezeka kuimbidwa mlandu wopezeka ndi galimoto yomwe akuganizira kuti inabedwa komanso kukhala ndi zikalata zachinyengo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.