Nkhondo ya Russia, Ukraine yakhudza mitengo yazinthu kuno – boma

Advertisement

Boma la Malawi kudzera kuunduna wa zamalonda lati chimodzi mwa zinthu zomwe zapangitsa kuti mitengo ya zinthu ikwere mdziko muno ndi nkhondo yapakati pa dziko la Russia komaso Ukraine yomwe akuti yasokoneza ntchito za malonda padziko lonse.

Izi ndi malingana ndi nduna yoona za malonda a Mark Katsonga komaso nduna yazofalitsa nkhani a Gospel Kazako omwe amayankhula lachitatu mumzinda wa Lilongwe, komwe maundunawa anachititsa msonkhano wa atolankhani.

Malingana ndi a Katsonga, kukwera mtengo kwa katundu wambiri m’dziko muno ndikaamba ka nkhondo yomwe ikuchitika pakati pa Ukraine komanso Russia ati chifukwa choti katundu wambiri ochokera maiko akunja akukhala okwera mtengo kaamba kankhondoyi.

Pothilira ndemanga za nkhaniyi, nduna yazofalitsa nkhani a Gospel Kazako ati ndizachidziwikile kuti dziko lino likuyenera kukumana ndimavuta pazachuma ati kaamba koti nkhondo ili ngati mtsinje omwe umatha kusefukira ngakhale mvula itabwera kumtunda kokha.

“Nkhondo ili ngati mtsinje, mvula imatha kuvumba kuntunda kokha koma anthu akumusi amatha kulephera kuwoloka mtsinje ndipo anthu akumusi amadabwa kuti zatheka bwanji kuti mtsinjewu wadzadza osadziwa kuti mvula inabwera kumtunda kokha.

“Ndichimodzimodzi ngati momwe zikuchitikira panopa ku Russia ndi Ukraine komwe akumenyana. Ife kuno sitikuva ngakhake chipolopolo chimodzi koma zikutikhudza ndithu chifukwa ikonome yadziko lapansi inakolanakolana, palibe ikonome yomwe inganene kuti imadziyimilira payokha,” atelo a Kazako.

Ngakhale zili choncho, nduna ziwirizi zati boma likuyesetsa kuyankhulana ndi maiko monga South Sudan komanso India pofuna kuliimbikitsa nkhani za malonda pakati pa maikowa ndipo ati akukhulupilira kuti ubalewu ukagwira msewu, zinthu zambiri ziyenda bwino.

Pamsonkhano omwewu, boma kudzera kwa ndunazi ladzudzulaso makampani ena opanga ndikugulitsa zinthu zosiyanasiyana mdziko muno kuti ena mwa iwo akukweza dala kwambiri mitengo yazinthu zina.

Apa ndunazi zinati zifufuza makampani onse omwe akuganizilidwa kuti akukweza dala mitengo yakatundu osiyanasiyana.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.