Alimi adandaula ndikupselera kwa mbewu kamba ka dzuwa

Advertisement

Ngakhale kuti mvula yayamba bwino m’madera ambiri m’dziko muno, alimi ochuluka akuti ali ndi nkhawa kuti sakolora zokolora zochuluka mchaka chikubwerachi kamba kakupselera kwa mbewu zawo zomwe anabzala ndi mvula yomwe ankayiganizila kuti itha kukulitsa mbewuzi.

Monga mwachizolowezi, alimi ang’onoang’ono okhala mdera lamfumu yayukulu Mkanda m’boma la Mulanje, ati iwo anabzala mbewu zawo ndimvula yomwe inagwa kumayambiliro kwamwezi wa disembala chaka chino pokhulupilira kuti mvulayi ikuza mbewu zawo monga mwazaka zonse.

Alimiwa ati chibzalireni mbewuzi, patha tsopano mwezi ndi sabata zingapo mvula osagwanso zomwe zachititsa kuti mbewu zambiri monga fodya komanso chimanga zipselere ndi dzuwa lolusa lomwe lakhala likuwala.

M’modzi mwa alimi okhudzidwawa yemwenso ndi khansala wadera la Mulanje Paseyani, a Daniel Chauluka, ati iwo ngati mtsogoleri ndiwokhudzidwa kamba kakuwonongeka kambewuzi zomwe akuti ngakhale mvula yayambanso sizingapulumuke.

“Ine ngati mtsogoleri, ndili okhudzidwa ndikupselera kwa mbewu makamaka chimanga chomwe chikupselera chitatulutsa kale ngalare. Sitikukayika kunoko kukhala njala yoopsa. Moti tikunena pano anthu ambiri akusowa chakudya m’manyumbamu zomwe ndichiopsezo chachikulu,” anatero a Chauluka.

Iwo anatinso ngati khansala, anayesetsa kukumana ndi akuluakulu owona za ulimi m’bomali kuti athandizepo ndi mbewu makamaka ya chimanga kuti panthawi ino yomwe mvula yayambanso kugwa alimi azule chimanga chomwe chinapselera ndidzuwa nkubzalanso china chatsopano.

“Ndinayesesa kuthamangathamanga kukumana ndi akuluakulu azaulimi kuti atithandize ndimbewu yachimanga yomwe tigwilitse ntchito tikazula yomwe inapselerayi. Tipemphanso boma ndi ena akufuna kwabwino atithandize ndithandizo lachakudya pakuti maanja ambiri kuno akuvutika ndinjala,” anatero a Chauluka .

Khansalayu anati akuluakulu azaulimiwa anamutsimikizila kuti abwera mdelari kuzazionera okha vutoli ndikupanga lipoti kuboma kuti athandize mwachangu. Iye anati pakalipano chiwelengero cha maanja omwe akhudzidwa ndivutoli mdelari ndipo ali mu ululu wanjala ndi oposera mazana atatu.

Malinga ndikhansalayu, delali limayamba kulandira mvula yoyamba yodalirika yomwe anthu amabzalanayo mbewu m’mwezi wa okutobala kumapeto komanso kumayambiliro kwa mwezi wa Novembala.

M’mawu ake, mfumu yaying’ono Kasiya, yemweso ndi m’modzi mwa alimi odziwika mdelari naye anatsimikizila zavutoli lomwe anati lakhudza kwambiri anthu okhala mdera lake.

Mfumu Kasiya inati anthu mdera la mfumu yayikulu Mkanda ali pavuto lomwe likufunika thandizo mwamsanga ponena kuti ngakhale mvula yayambanso palibe chomwe chingathandize ndimbewu zopselerazi ndipo kuti panopa ali pa kalikiliki ozula kuti abzalenso zina.

“Mdera lino la Mkanda tinadzala mbewu zathu moyambilira koma kunena zoona palibe chomwe taphula pakuti mbewu makamaka chimanga zapselera ndi dzuwa. Tili pachisoni chachikulu ndipo tili ndichikhulupiliro kuti kunoko kukhala njala yoopsa,” anatero a Kasiya.

Kafukufuku akuonetsa kuti chaka chino mvula yavuta m’madera ambiri m’’dziko zomwe akatswiri oona zakagwedwe kabwino kamvula akuti zitha kudzetsa njala mu chaka chikubwerachi.

 

 

Advertisement