Muneneze mabanki omwe akukudulani ndalama – Mlusu

Advertisement

Boma kudzera kwa nduna ya zachuma a Felix Mlusu lati anthu omwe akudulidwa ndalama zawo ku mabanki mu dzina la VAT, akanene ku banki ya Reserve kuti ndalama zawo zonse zibwezedwe.

A Mlusu amayankhula izi Lachiwiri kwa atolonkhani mumzinda wa Blantyre pomwe malipoti akusonyeza kuti mabanki ena ayamba kale kudula ndalama anthu pomwe akuchita zinthu zina ati kaamba kalamulo lomwe lakozedwa lokhudza nsonkho pa ntchito zina zamabanki..

Nkhaniyi ikutsatira kulengeza kwa bungwe la mabanki la Bankers Association of Malawi (BAM) lomwe sabata yatha linati mabanki onse azidula ndalama pazinthu zina zomwe anthu azipanga zokhudza banki zomwe mwa zina ndimonga potumizilana ndalama.

Koma bungwe lotolera msonkho la MRA lanadzudzula mabankiwa ati ponena kuti lamulo lomwe lakonzedwa la msonkho, silikukhudza makasitomala koma mabanki okha.

Mabankiwa sanavere langizoli ndipo patangodutsa ma ola ochepa, mabanki ambiri anayamba kutumuzira makasitomala awo mauthenga owadziwitsa kuti kuyambila pa 1 November, adzidulidwa 16.5% pa ndalama zawo pantchito zina za banki.

Tikunena pano mabanki ena ayamba kale kudula anthu ndalama pomwe akutenga ndalama kudzera pa ATM komaso potumizira anzawo ndalama zomwe a Mlusu aati ndizolakwika kwambiri komaso ndikuphwanya malamulo.

Iwo awuza anthu kuti akanene kubanki yaikulu ya Reserve ngati adulidwapo ndalama pomwe amachita chili chonse chokhudza banki.

“Tikufuna tichenjeze kuti zomwe akuchita mabanki poika msonkho wa 16.5% kwa makasitomala ndikumawadula ndalama zawo, ndizolakwika komaso ndikuphwanya malamulo ena okhudza msonkho.

“Nde ife tikuti ngati alipo amene zamuchitikira kale izi kuti wadulidwa ndalama ku akaunti yake pomwe amapanga chili chonse, akanene za nkhaniyi ku banki ya ikulu ya Reserve ndipo ndalama zawo zonse zomwe adulidwa zidzabwezedwa,” atelo a Mlusu.

Pakadali pano a Malawi ambiri awonetsa chidwi chotsekula ma akaunti awo ku banki ya FDH kaamba koti ndiyokhayo yomwe yakanitsitsa kuti sizidula makasitomala ndalama iliyose pomwe akupanga chili chonse

Advertisement