Coronavirus: anthu 25 amwalira m’maola 24 apitawa

Advertisement
Chiwerengero cha anthu omwe akumwalira ndi kachirombo ka corona chikunka chikukwelerabe pomwe m’maola 24 apitawa anthu 25 ndi omwe atisiya atadwala matendawa.

Izi ndimalingana ndi nduna yazaumoyo a Khumbize Kandodo Chiponda omweso ndi wapampando wakomiti yamtsogoleri wa dziko yoyang’anira ntchito yothana ndi mlili wa covid-19.

A Kandodo Chiponda omwe amayankhula Lachinayi madzulo pomwe amalidziwitsa dziko mmene zinthu zilili, anati ndizokhumudwitsa kuti chiwerengero cha anthu omwe akupezeka ndikachilomboka chikukwerabe.

Iwo anati mmaola 24 apitawo, mwa anthu 3,229 omwe anayezedwa, anthu 785 atsopano ndiomwe apezeka ndi matendawa pomwe anthu 444 atsopano ndi omwe achira komaso anati anthu 25 atisiya.

A Chiponda anaonjezera kuti anthu 60 atsopano ndi omwe agonekedwa mchipatala pamene anthu 36 atsopano ndi omwe atulitsidwa mchipata momwe anagonekedwa pomwe amadwala matendawa.

Apa ndunayi yapempha anthu mdziko muno kuti apitilire kutsatila malangizo omwe unduna wa zaumoyo ukupeleka ndi cholinga chofuna kugonjetsa matendawa komaso alimbikitsa onse omwe apezeka ndi matendawa kuti asamadere nkhawa.

“Chiwerengero cha odwala matendawa chikukwera kwambiri ndipo ndizokhumudwitsa kuti kufika pano tataya azibale athu ochuluka. Taona kuti anthu tsopano ayamba kukhala ndimantha kaamba kamomwe matendawa akufalira pakati pathu.

“Komano ndimafuna ndinene kuti kupezeka ndimatendawa sindiye kuti wafa kale, ayi sichoncho. Matenda wa titha kuwagonjetsa ngati tingapitilire kutsatila njira zonse zopewera zomwe azachipatala akutiuza,” atelo a Kandodo Chiponda.

Apa ndunayi yati ndikofunika kwambiri kuti anthu azithamangira kuchipata pomwe akuva zizindikilo za nthendayi osati kudzipatsa okha mankhwala zomwe anati zamathaso kuika pachiopsezo miyoyo yawo ponena kuti ndiachipatala okha omwe amadzi mulingo wa mankhwala oyenera kumwedwa.

Kuyambira pachiyambi kufikira pano, anthu 41,498 ndi omwe apezeka ndi kachiromboka, anthu 1,301 amwalira, anthu 34,583 achira kumatendawa, pomwe anthu 5,382 ndi omwe akudwalabe ndipo ena 220 ndi omwe agonekedwa mchipatala.

Pakadali pano katemera wa covid-19 wa AstraZeneca okwana 192,000 yemwe amayenera kufika mdziko muno Lachinayi, walephera kufika kaamba kazovuta zina ndipo malingana ndi a Kandodo Chiponda tsiku lobwera katemerayu silinadziwike.

 

Advertisement