Chiwelengero cha opezeka ndi Corona chafika pa 70

Advertisement

Chiwelengero cha anthu omwe apezeka ndikachilombo ka Corona komwe kakumayambitsa matenda a COVID-19 chafika pa 70 tsopano ku Malawi.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi nduna ya zaumoyo m’dziko muno a Jappie Mhango omwe amayankhula lamulungu pa msonkhano wa atolankhani ku Mzuzu komwe analengeza kuti anthu ena asanu apezekaso ndikachilombo ka Corona.

A Mhango ati mwa anthu asanuwa, m’modzi ndiochokela ku Zomba pamene ku Lilongwe kwapezeka awiri komanso ku Blantyre kwapezeka awiri omwe ali ndi kachilimboka.

Iwo ati chosangalatsa nchakuti anthu ena atatu achira ku nthendayi zomwe zapangitsa kuti chiwerengelo cha anthu ochira chifike pa anthu 27 ndipo anthu omwe akudwalabe nthendayi mpaka pano alipo 40 tsopano.

Ngakhale chiwerengero cha anthu omwe akupezeka ndikachilombo ka Corona chikukula, pakadali pano chiwerengero cha anthu omwe amwalira ndi nthendayi chidakali pa atatu.

Apa ndunayi inati izi ndizosangalatsa kwambiri potengera kuti mu maiko ena anthu mazana mazana akupitilirabe kumwalira ndinthendayi.

Ndunayi yati pakadali pano madotolo akupitilirabe kumayeza anthu omwe akuganizilidwa kuti ali ndikachilomboka ndipo alangiza anthu m’dziko muno kuti apitilize kutsatila malangizo omwe undunawu ukumapeleka pofuna kupewa kutenga kachilomboka.

Pakadali pano, Ku Lilongwe kwapezeka anthu 28 kuphatikiza imfa yamunthu mmodzi pamene ku Blantyre chiwerengero cha omwe apezeka ndi kachilomboka chafika pa 18 kuphatikizaso imfa yamunthu mmodziso.

Ku Thyolo kwapezeka odwala nthendayi 9, pamene 5 apezeka m’boma la Nkhata bay, atatu ku Mzuzu, awiri ku Zomba ndipo maboma a Chikwawa, Nkhotakota, Karonga, Mangochi ndi Mulanje konseku kunapezeka odwala matenda a COVID-19 m’modzi m’modzi.

Advertisement