Namadingo aputa mavunkhomola

Namadingo blasts Bushiri in new song

Oyimba odziwika bwino Patience Namadingo waputa mavunkhomola atanena kuti oyimba nzake Lulu sanafike mu gulu la oyimba otchukitsitsa komanso omwe sadzaiwalika mpaka kalekale m’dziko muno.

A Namadingo ananena izi masiku apitawa pa tsamba la mchezo la Fesibuku.

Iwo anati Lulu, yemwe imodzi mwa nyimbo zake zotchuka ndi Mbambande, ndi oyimba bwino koma sanafike pokhala oyimba oti azadziwika mpaka kalekale mu Malawi muno.

“Lulu ndi namatetule wa panopa. Koma sitingamuike mu gulu la oyimba osaiwalika ngati Lucius Banda and Billy Kaunda,” anatero a Namadingo omwe chaka chino anajambulaso nyimbo zina za a Banda ndi a Kaunda mu chamba cha reggae.

Iwo anaonjezera kunena kuti oyimba osaiwalika ndi omwe nkhani zawo zimakhala ngat nthano zomwe makolo amauza mibadwo inayo.

Kulankhula kwa a Namadingoku kwautsa mtsutso pa masamba a mchezo pomwe aMalawi ena a kugwirizana nawo pamene ena akutsutsa.

Ena otsutsana ndi a Namadingo akuti munthu amakhala oyimba otchuka kapena osaiwalika ngati ali odziwika bwino kwa mbadwo umodzi okha ndiye Lulu ali mu gululi.

Ogwirizana ndi a Namadingo akuti Lulu sanafikepo chifukwa oimba osaiwalika ndi okhawo omwe anatchuka achinyamata a nyengo ino asanabadwe.

 

Advertisement