Boma lati liyesetsa kuti mu ndondomeko ya zachuma ikubwerayi aikemo zinthu zomwe zikomere anthu ochuluka mdziko muno.
Izi ndimalingana ndi nduna yazachuma a Joseph Mwanamvekha omwe amayankhula mu mzinda wa Blantyre pakutha pa mkumano omwe amafuna kumva maganizo a anthu pa zinthu zomwe zikuyenera kuikidwa mu ndondomeko yazachuma ikubwerayi.
Atalandira maganizowa, a Mwanamvekha anati ayesetsa kuti mu budget yomwe ikhalepo mwezi wa mawa ku nyumba ya malamulo aikemo zina mwazinthu zomwe anthu apempha pa mkumanowu.
Mwazina anthu apempha ndunayi kuti iwonetsetse kuti mu bajeti ikubwerayi, boma liyike ndalama zapadera zomwe zithandize kutukula achinyamata omwe akusowa ntchito atamaliza maphuzilo komaso anthu apempha kuti boma litsitse mitengo yazinthu zofunika zina ndi zina yomwe yakwera posachedwapa.
“Choyambilira ndithokoze onse omwe anabwera kuzapereka maganizo awo pandondomeko ya zachuma ya mwezi wamawa ndipo nditha kunena mosabisa kuti monga zimachitikira m’madera mwina monse, kuno ku Blantyre mkumanowu wayenda bwino kwambiri.
“Mwazina anthu atiuza kuti tikuyenera mu budget ikubwerayi kuti tiganizile achinyamata omwe sanalembedwe ntchito. Tauzidwaso kuti titsitse mitengo yazinthu zina zofunika ngati buledi, shuga, mafuta ndizina zotero yomwe yakwera. Nde ife tikuti tamva mapemphowa onse omwe aperekedwawa ndipo tiona kuti titani,” anatero a Mwanamvekha.
Pamkumano omwewu anthu anapemphaso boma kuti liyesetse kuthetsa mchitidwe wa katangale omwe ati umapangitsa kuti chuma cha boma chizisakazidwa ndipo ati izi ndizomwe zikubwezeretsa dziko lino m’mbuyo pazachuma.
Undunawu wauzidwaso kuti uyesetse kuchepetsa ngongole zomwe dziko lino limatenga m’maiko akunja komaso kumabanki akonkuno ndipo apa boma lauzidwaso kuti lisiye kudalira kwambiri bank ya Reserve ponena kuti izi zimabwezeretsa ntchito za bankiyi m’mbuyo.
Pamkumanowu panali nthumwi za mabungwe osiyanasiyana pankhani ya zachuma mdziko muno monga MCCI, Indigenous Business Association of Malawi (IBAM), akuluakulu a masukulu aukachenjede ndi ena ambiri.