Mu Meyi tikuchotsa a Chilima osati kusintha boma – Uladi Musa

Advertisement

Yemwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) mchigawo chapakati a Uladi Mussa ati chisankho chikubwera mwezi wa mawachi sichoti anthu asinthe mtsogoleri wadziko koma ndichoti dziko lino lichotse pa mpando a Saulos Chilima.

A Mussa amayankhula izi lamulungu lapitali pamisonkhano yoyimayima yomwe mtsogoleri wa dziko lino, a Peter Mutharika anapangitsa m’boma la Nkhotakota.

Mussa: Tikuchotsa a Chilima

Iwo anati dziko lino silimayenera kupangitsa zisankho kaamba kautsogoleri wabwino wa a Mutharika koma zisankhozi zichitika ndicholinga chofuna kungokwanilitsa malamulo adziko lino omwe amati zisankho ziyenera kuchitika pakatha zaka zisanu zili zonse.

Iwo anatsindika mfundo yawo kuti cholinga china cha zisankho za chaka chino ndikuti anthu asankhe aphungu komaso makhansala achipani cha DPP m’madera omwe munali azipani zina komanso kuchotsa Chilima paudindo wake wa wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino.

Iwo anati a Chilima omwe akulandirabe ndalama m’boma koma osagwira ntchito akuyenera kuchotsedwa pa udindo wawo ngati wachiwiri kwa ndikuikapo a Everton Chimulirenji.

M’mawu awo omwe akuimilira chipani cha DPP pa mipando ya uphungu wa nyumba yamalamulo m’bomali omwe ndi a – Henry Chimunthu Banda, Martha Lunje, Grezelder Jeffrey komaso a Brenda Saidi Banda – anathokoza boma kaamba kofikitsa zitukuko zosiyana siyana m’bomali.

Iwo analonjeza kuti akasankhidwa pa zisankho zikubwelazi, apitiliza kufikitsa chitukuko m’bomali ndipo ati amanga, misika, malo okwelera magalimoto, sukulu komaso ati akumba mijigo yochuluka m’bomali.

Advertisement

3 Comments

  1. Ala zopanda mutu. Mukukanika kutipatsa chitukuko cholezeka, what you know is just to speak. Boma la DPP ndikanakhala mulungu ndikanakuotchani ndi katatu kuposa chimwa ena onse. Up to now am failing to imagine how can a normal government construct a maize storage and proudly calling it a Kamuzu International Airport Terminal !!!

Comments are closed.