Ati muziliyatsa la mtondo wadooka mukangomva za tambala wakuda. Ati pali Kongeresi, a Malawi nonse muzipita kukabisala ndithu osati kuthamangilako.
A Nicolas Dausi amene ndi nduna yoona zofalitsa mauthenga komanso mneneri wa boma anauza msonkhano ku Mpherembe mu boma la Mzimba kuti chipani cha Kongeresi sichosewela nacho.
Pa msonkhanowo umene anachititsa ndi a Peter Mutharika, a Dausi anati Kongeresi simalabadila lonse anthu a kumpoto.
“Inetu paja ndinali komko ndinachita chothawa. A Malawi, Kongeresi si chipani chomachiyikila kumtima. Tsankho ndiye kudya kwawo,” anatelo a Dausi.
A Dausi anaonjezelapo kuti mu masiku a Kamuzu, ma unduna a zachuma ndi ntchito sakanaloledwa kuti apite kwa munthu ochokela ku mpoto kamba ka tsankho.
“Koma taonani lero, a nduna a zachuma ndi a Goodall Gondwe pamene a Jappie Mhango ndi a nduna a zantchito,” anatelo a Dausi.
Polankhulapo a Gavanala a DPP a ku chigawo cha kumpoto a Kenneth Sanga anati chipani cha DPP chisesa mipando yonse ya uphungu mu boma la Mzimba kamba koti anthu ndi okondwa nacho chipanichi.
Anthu akumpoto ndiwo atsango latadzaonani osati Malawi Congress akunama
A DAUSI…. Ndinu munthu omvetsa Chisoni…