A Mutharika ali ngati Yesu – Mchacha

4

Inu owelenga Baibulo, mwaikumbukila nkhani ya bulu anakwelapo Yesu ija akukalowa mu Yerusalemu? Ngati mwayiwala, dikilani tikukumbutseni.

Paja Yesu anatuma ophunzila kuti apite mmudzi, ndipo akapezamo bulu ndipo akamumasule ndi kumupititsa kwa iye. Aliyense akafunsa, iwo anene kuti akumufuna ndi Yesu.

Charles Mchacha

Mchacha

Izi anachitadi ophunzila. Ndipo Yesu anakwela bulu ameneyu polowa mu Yerusalemu.

Gavanala wa chipani cholamula wati a Mutharika ali ngati Yesu mu nkhaniyi ndipo ena onse ogwila nawo ntchito ali ngati bulu amakambidwayi, inde kuphatikizapo a Chilima.

Gavanalayu a Charles Mchacha amayankhula izi pa msonkhano omwe anachititsa a Mutharika ku Lirangwe mu boma la Blantyre.

A Mchacha anati monga anthu anayalila zovala bulu uja kuti adutsepo kamba ananyamula Yesu, anthu pano amakonda a phungu kudzanso nduna za DPP kamba zanyamula a Mutharika.

“Kapangitseni msonkhano wanu muone kuzakhala opanda munthu,” anatelo a Mchacha.

Share.

4 Comments

  1. Nanu inu atidye nawo opusa inu, cant you see that man muthalika mukumupitililitsa pa yesu? Yesu was humble and he was walking on foot, he didnt own even a donkey man pitala analanda chuma chamasiye pameme yesu was feeding the poor, nde wekha sungaone kusiyana ngati uli wabwino bwino?

  2. If he had nothing to say he should have kept quiet,Jesus is God …..He must go back on air to apologise to the Nation and to Mutharika,their dirty politics aren’t like anything good biblical…May God forgive him….people are like a beast Jesus rode.. God forbid

  3. It’s not surprising cos Nchacha is not that educated that he can understand things but anyway I can forgive him cos he was talking all these for the sake of his stomach. The only problem in this story is to put Mutharika in the same sentence with The Lord Jesus Christ. For his own information Ngumuya won his seat after beating DPP candidate. So it’s not all about DPP. The other thing he must remember that kunali, a Charles Kamphulusa, MHSRIP, a Mpombwe, a Davies Kapito MHSRIP, a Chikakwiya MHSRIP. How did their political lives ended???? Mau a Mulungu amatiphunzitsa kuti Do Not Be Fooled God Can Never Be Mocked so be careful. I’m not saying he must agree with thoseveral who want Chilima no, democracy is about debate, arguing. Opposing, agreeing, disagreeing but he must choose his words cleverly.

%d bloggers like this: