Tisakuoneni ku mpira lero – Noma, Bullets iuza Sulom

Advertisement
BB-vs-Noma-TNM

Ngati muli akuluakulu a bungwe lija la Sulom, ati chonde lero zipumi zanu zisaoneke ku Bingu National Stadium kumene maule apalane mamba ndi nyerere.

Malinga ndi chikalata chimene a Malawi24 anapatsidwa chosayinilidwa ndi mkulu wa timu ya Bullets a Konrad Buckle komanso wapampando wa ma trustee a noma a Rashid Gaffar, akuluakulu a Sulom sali olandilidwa ku masewelo a lero.

BB-vs-Noma-TNM
Aakuluakulu a Sulom sali olandilidwa ku masewelo a lero.

“Akuluakulu a matimu a Nyasa Big Bullets ndi Beforward Wanderers ndi okhumudwa ndi zipongwe zimene atsogoleri awo anachitidwa ku Mangochi pamene kunali msonkhano waukulu wa Sulom,” chatelo chikalatacho.

Chikalatacho chapitilila ndi kunena kuti kamba ka chipongwe chomwe anachitidwa atsogoleri a matimu awiriwa, masapota a matimuwa ndi okwiya ndipo akufuna kubwenzela chipongwe.

Atsogoleri a matimuwa ati iwo ndi ofooka kuti akaletse masapota awo kubwenzela chipongwe.

Pofuna kupewa zonsezi, iwo apempha akuluakulu a Sulom kuti asapite ku masewelowa poopa kuona mbonaona.

Sabata zinayi zapitazo, atsogoleri a matimu a Bullets komanso Noma anaombedwa timakofi ta msinkhu wao ku Mangochi pa msonkhano waukulu wa pa chaka wa Sulom.

Dzingandanga zimene zidachita chipongwe akuluakulu awa ati zidatumidwa ndi Sulom.

Advertisement