Kaya muli chani m’chuinomu choti mpaka ndi kufika poimitsa maphunziro kenako sukulu ndi kutsekedwa ndithu?
Ma lipoti amene Malawi24 yalandila aonetsa kuti sukulu ya za ulimi ya Mwimba ayamba aitseka kaye.
Ati akulu akulu a pa sukuluyi aganiza zoitseka zitadziwika kuti aphunzitsi a pa sukuluyi achulutsa kugona ndi ana awo a sukulu. Maka mowakakamiza.
“Olo uyankhe molondola mafunso, amatha kukulepheretsa ndi cholinga choti ugone nawo basi,” anatelo ophunzila wina kunena za aphunzitsi ake.
Malawi24 yauzidwa ndi anthu angapo kuti linasanduka khalidwe pakati pa aphunzitsi kuti azivula ndi kumagona ndi ophunzila awo. Ndipo ophunzila ambiri amavomela poopa chilango.
Khalidwe la aphunzitsi kumagona ndi ophunzila awo maka mu ma sukulu a ukachenjede lakhala likumveka kwambiri pa Malawi.