JB atha kufikila m’manja mwa a Polisi

Advertisement
Joyce Banda

Nkhani ija ya ndege ija, zija anamutchula a Lutepo zija, mwinanso zija adanena a Kasambara zija.

Mneneri wa a Polisi mu dziko muno a James Kadadzera ati chilolezo chomwe a Polisi adatenga chowapatsa mphamvu yonjata Mayi Joyce Banda chidakalipo.

Joyce Banda
Mayi Joyce Banda atha kumangidwa ndi apolisi akafika mdziko muno.

A Kadadzera auza olemba nkhani kuti lingaliro lonjata a Banda silidathe chifukwa iwo anakhalitsa kunja.

“Chilolezo chija chilipo ndithu ndipo ndi champhamvu ngati kale,” anatelo a Kadadzera.

Mayi Banda alengeza kuti akubwera kumapeto a sabata ino.

Chaka chatha a Polisi adalengeza kuti atenga chilolezo chowapatsa mphamvu yonjata Mayi Banda kamba koganizidwa pa milandu ingapo.

Advertisement