A Mutharika akulingalila zonyonga onse okupha ma albino

Peter Mutharika

Wamisala anaona nkhondo. Ataopseza kuti ayenda buno bwamuswe pofuna kukakamiza boma la Malawi kuti lizinyonga anthu onse opezeka kuti apha albino, a Winiko akuoneka ngati tsopano atha kumvana Chichewa ndi Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika.

Chikalata chimene atulutsa a ku nyumba ya boma chaonetsa kuti Mtsogoleri wa dziko lino tsopano akulingalila ngati zingakhale zothandiza kuti azinyonga anthu onse opezeka kuti apha munthu.

Peter Mutharika
a Mutharika akulingalila ngati zingakhale zothandiza kuti azinyonga anthu onse opezeka kuti apha munthu.

Chikalatachi chatulutsidwa pamene a Malawi atutumuka ndi kuphedwa kwa a Mcdonald Masambuka mu boma la Mangochi.

A Masambuka anali munthu wa chi albino ndipo anaphedwa ndi anthu amene amakhulupilila zopusa zoti mafupa a Bambo Masambuka angawalemeretse.

A Mutharika mu chikalatachi alonjeza kuti ngati boma iwo achita zotheka kuti anthu onse okhudzidwa ndi imfa ya a Masambuka abweletsedwe pa Khoti ndi kulandila chilango choyenela.

A Mutharika aonjezelaponso kuti anthu akufunika kukambilana moona mtima pa nkhani ya chilango chonyonga kwa anthu onse opanga chipongwe anthu a chialubino.

Advertisement