Iwalani zotenga boma a Kongeresi, anthu kummwera sakukudziwani ndi komwe – Mpinganjira

Advertisement
brown-mpinganjira

Wamasuka tsopano m’busa Brown Mpinganjira. Wayambapo zija zokhuthula mawu pa misonkhano yandale. Nkhani pano si ya PP anaisiya ija koma ya DPP. Ndipo iye wachenjeza anthu a kummwera kuti asazayese kuvotela Kongeresi.

Amene anali wachiwiri kwa President wa chipani chotsutsa cha PP a Brown Mpinganjira anenetsa kuti 2019, chipani cha DPP chikupitiliza kukhala m’boma.

brown-mpinganjira
Mpinganjira: Chipani cha DPP chiipitiliza kukhala m’boma.

Polankhula ku Phalombe kumene kunali msonkhano wa chipani, a Mpinganjira anenetsa kuti otsutsa a Kongeresi alibe kuthekela kochotsa DPP.

Iwo anati chipani cha MCP ndi cha anthu a tsankho ndipo atati apambane lero, iwo sangaganizile ndi komwe anthu a kummwera.

“Kuno ku Phalombe, MCP siyimikako munthu ndi komwe. Mukuti amenewa kupambana angakuganizileni ndi komwe, adziwa bwanji zokhumba zanu?” anatelo a Mpinganjira.

Pa msonkhano omwewo, a Mpinganjira analandila anthu oposa 400 amene amati achoka ku chipani chawo chakale cha PP.

Iwo anati PP tsopano yatha ndipo anthu asamakakamilebe ngalawa yomila ndi madzi ngati imeneyo.