Zilibe ndalama nyerere: miyezi yatha tsopano osalipila ma Kochi

124

Apambana ligi, kawiri konse kufika mu ndime yotsiliza ya mipikisano ndipo akukamba zopita ku mpikisano wa CAF koma manoma ali ndi mthumba moyela.Maluzi ngati khoswe wa mu kachisi.

Super League Malawi

Osman: Ndalama zathu sakutipatsa mwezi ukatha.

Malinga ndi malipoti, akatswiri a ligi chaka chino a nyerere ati akulephela kulipila aphunzitsi a timuyi ngakhale kuti apambana ligi komanso akukhalila chithumba cha ndalama cha kampani ya ku Japan ya Be Forward.

Malipoti amene anatsindikidwa mu nyuzipepa anaulula kuti aphunzitsi a noma akhala asakulandila chawo cha pa mwezi kuchokela mu mwezi wa August.

Mphunzitsi wamkulu ku noma, a Yasin Osman anatsimikiza kuti chioneleni malipiro awo mwezi wa August, kwinaku angokhala kamba kokonda timu.

“Pano sitikudziwa kuti nkumakhala bwanji koma za ndalama izi ndiye ah sakutipatsa zathu mwezi ukatha,” anatelo a Osman pouza olemba nkhani.

Ndipo akuluakulu a timuyi nawo anatsimikiza kuti kuli maluzi ku Lali Lubani kumene amene akuwakanikitsa kulipila aphunzitsi awo.

“Koma tikulongosola zimenezo. Inu mtima m’malo. Pompano ayimba lokoma aphunzitsi amenewa,” anatelo wapampando wa nyerere a Gift Mkandawire.

“Anthu amvetse kuti chithandizo chochoka ku Be Forward chimapita ku malipiro a osewera basi, aphunzitsi siziwakhudza ndiye timayenela kulongosola zimenezo tokha,” anatelo a Mkandawire.

Iwo anaonjezelapo kuti Mmbuyomu nyerere zakhala zikudalila anthu akufuna kwabwino ndi kangachepe kotola ku masewelo kuti alipile aphunzitsi awo.

“Ndiye pakati apa masewelo athu anali ndi ana basi, osatibweletsela phindu lenileni,” a Mkandawire anamaliza choncho.

Share.

124 Comments

 1. Makochi,mukhaliranji kumalo omwe alibe malipiro?Ndinu makochi abwino,azeru,ntchito olimbika,koma taonani tsikulina mugona osafunda pakuti timu akuti ndi mphembedzu,sidakupatseni zanu.Pepani musauka ngati timuyi.Noma mukuti mukamenya CAF,ndalama zake mubela ndani?usiwatu umeneu.Ndikakhala ine ndinenekuti Maule!!!Maule!!!Maule kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk aaa koma awa!!!

 2. inuyo dekhani and muzalembeso team ikamazanyamuka kupita kokamenya CAF muzayaluka inu mmaleka kupitako inuo ma team anu ali ndi ndalamawo bwanji mwikho basi demeti

 3. kkkkkk hahahahaha pwetepwetepweteeeeee masapota anoma anya lero tidakuuzan akapado inu kt malonda amagalito mngosadalilika umatha miyezi kt ugudwe taonani lero mukugoneka ana ndinjala ndiye winawe ukutukwana chani yambani geni yafodya simanama onani kubullets anzanu akudyelela naye kampopi

 4. Hahahaha Noma for Life wanzeru wanena kale apa kuti asiyeni aziona okha ndipomwe ena mukutha mau neba neba neba bus yako ilikuti neba? Kkkkkkkkkkkkkkkkkkiest

 5. I wonder some people are saying is a fabricating story but frankly speaking Noma ilibe ndalama , ndiye ati kulowa caf koma ndikukayika ngati mukapezeko ndi draw yomwe mutengeko matumba ambiri muzikapakira mtibwi wazigoli omwe mukatutezo .nonsense!!!

 6. Ine ndiwa ma banker koma to say the truth nyerere ndalama zilibe mwina mongukumbusana chabe yitamenyedwa derby mu tnm nyerere zitaluza zinakana kunyamuka kubwerera ku BT, yitamenyaedwa Carlsberg cup nyerere zinakanaso training eti malipiro sanawapase nde…. ine palibe chachilendo pa nkhaniyi awa ndalama alibe and kupita ku caf aaaaa kuputa mavuto uko….kaya winawe ukwiya koma zomwe ndafotokoza apa ndizoona ndithu….ma bankers more fireeeeee tiwonane Saturday pa BNS

 7. It’s funny some Wanderers fans they are backing their team. Kma that’s the truth alibe ndalama awa coz I saw mu the nation yapa boxing day. The club is broke hahaha. Ajoine bank mukhonde awa

 8. #Neba Watenga Ligi Cuz Of Osman As Head Coach Nde Muziti Alibe Ndalama Lero? Nthawi Yoseyi Samanena Bwanji Anthu Akupita CAF? Tiona Mathero Ake.

 9. Ndiwe Galu basi zilibe ndalama Makolo ako akufa njala kumudzi kwanu ukufuna kuti namidza kuti MANOMA alibe ndalama ndiosokonekela mutu usiyechamba wachiyacho wasowa zolemba mutu wako

 10. Kanyimbi ameneyu anangobadwa mayi ake ndikukamutaya mu chimbudzi mwayi ntchentche zinagwilizana ndikumutulutsamo,moti chakudya chomwe anayamba kudya anali manyi a mchimbudzi muzimukhulukila palibe chanzelu chomwe angalembe

 11. kod ngat simunawalipire ma coach ndi ma players ena asakambe chilungamo kod ,koma ikanakhala zapangidwa ku bb komaso ku bankers anoma apa mukuchita kuyadamula kukamwa ngat mvuwu kuli kuseka ndi kunyokodola azanu pano izo mwayamba kupsa nazo mtima Kklkkkkkkkkkkkkkkkkkk musovenge atah

 12. Shame on you admn, your all imbecile for reporting fabricating story. Just talk until you get tired, maybe you feel jealous with nyerere ?. Abwampini inu , achule, atombotombo, mitu zidangokula kma zilibe nzeru.

 13. Yaaaaaaaaa. tizivankhani. zonthakuka. ngatizimenezi eeeeeeeeee. ndimadabwakuti. chakachi. chikutha. wosava. khani. yazelu. ngati. iyi. Hahahaha. Kkkkikkkkikkki kekekekek. Mmmmmm. Koma. Zinazi

%d bloggers like this: