Ife tikuti kunsewu toto – atero ophunzira

235

Ophunzira msukulu zaukachenjede mdziko muno atemesa nkhwangwa pamwala kuti sapita nawo ku msewu kukachita zionetsero sabata lamawa.

Bungwe loyang’anira zipembedzo mdziko muno la Public Affairs Committee (PAC) lamema anthu kukachita zionetsero lachitatu likudzali pofuna kukakamiza boma kuti likonzeso malamulo oyendetsera zisankho mdziko muno.

Chanco students

Ophunzira msukulu za ukachenjede ati satenga nawo mbali pa zionetserozi.(File)

Mipingo yambiri yaonetsa chidwi chokapezeka kuzionetserozo zomwe malingana ndi bungwe la PAC zidzakhala za mtendere ndipo mipingo monga Anglican komanso Katolika kungotchula yochepa yamema oyitsatira kuti azatenge nawo mbali pazionetserozi.

Fisi anakanadi msatsi; Ophunzira msukulu za ukachenjede za Chancellor College komaso Polytechnic omwe ndimasukulu amene amadziwika bwino ndikupanga zionetsero ati iwo satenga nawo mbali pa zionetserozi.

Izi ndimalingana ndichikalata chomwe ophuzila msukuluzi atulutsa chomwe otikitila wake anali mlembi wagulu lina lomwe likutchedwa ophunzira okhudzidwa, a Chrispin Mahara.

Gulu la ophunzira okhudzidwali lati iwo ngati achinyamata okonda dziko la Malawi komanso odzipereka pa chitukuko cha dziko lino, asankha kusakhala chete koma kuyankhulapo pa nkhani zimene zamanga nthenje m’dziko muno makamaka pa zionetsero zimene zakonzedwa ndi PAC.

Iwo ati ngati achinyamata, ali okhudzika ndipempho loti akayende nawo pamsewu pa 13 disembala, pofuna kukakamiza boma kuti likonzenso malamulo oyendetsera zisankho m’dziko muno.

“Ife sitikutsutsana ndi ganizoli, koma ngati a Malawi komanso achinyamata omwe tili odzipereka kumpingo tili ndi mantha ngati nkhosa zokaphedwa pazifukwa izi: Sitinaiwale imfa yomvetsa chisoni ya a Malawi anzathu 19 amene anaphedwa, 58 amene anaombeledwa ndi ena ochuluka amene anavulazidwa modetsa nkhawa chifukwa cha zionetsero zonga zoterezi pa 20 Julaye, 2011.

“Tikudziwa kuti iwo ngati azitsogoleri mwina amvetsetsa kuti malamulo akufunikawo ndiotani ndipo ubwino wake ndi otani, koma adziwe kuti anthu ochuluka sakudziwa bwino za malamulowa. Kodi a Malawi ndi owapindulira motani? Pa chifukwa ichi nzotheka kuti pazifukwa zokomera iwo okha akufuna anthu aluze miyoyo, akatundu ndi tsogolo pa mfundo zimene mwina a Malawi ena alibe nazo vuto,” latelo gawo lina la kalatayo.

Ophunzirawa alangizaso a Malawi kuti asalore kuti kukhulupirika ndi kudzipereka kwawo ku mipingo yawo yosiyana kutengeredwe pa mgong’o.

Iwo ati ngati achinyamata amene anadalilidwa kuti apitilize maphunziro a ntchito zosiyanasiyana akupempha a PAC apeze njira ina yabwino koma zowatengera ku msewu ayi.

“Mzako amadutsa apa wagwa ndipo watchola mkono, wa nzeru podutsa amalambalara m’mbalimo. Pa 20 Julaye 2011, zoopsya tinaziona, mizimu ya anyamata anzathu ikukumbutseni china chake. Ife tasankha kulambalara m’mbalimo, tikuti kumsewu toto,” atelo ophunzira okhudzidwawa.

Share.

235 Comments

 1. yeboh sitingayende kunsewu pankhani yandale pomwe ya fees mutchalitchimo simunaikambe tikuvutika ndi mafees okwera koma PAC sinakambepo n’khale pang’ono

 2. Zaziii malo mokatsila feteleza koma ku nsewu, AAA ndakana mbuzi a PAC mbuzi omwe azapite kumsewu azalandilanso mbuzi zokhazokha kkkkkjj

 3. Anso a Malawi24 don’t know kuti protest or demonstration is enshrined in the Constitution of the Republic of Malawi. Malawians are free and it is their right to demonstrate, without fear or favor, just as iwowo a Malawi24 have the right to write without fear or favor. Let the Malawian people exercise their birthright without threats. Chivuta iwo a Malawi24 ndi chiani?

 4. Asapitedi awa, amakonda kuononga ndikuphwanya katundu, zinyumba, magalimoto a anthu opanda mulandu, ndi zina zotere, safuna zinthu za zeru awa. Asapitedi.

 5. Zionetsero siza ana sukulu.
  Ndiye zisawakhudze.
  Izi ndi za ife amalawi ozindikira mogwirizana ndi a PAC.
  Thanks Jaman for ur update.

 6. Then you will heard Police Shoot dead several people A, B, C, D,

  But failing to go and shooting with their count attack Mozambique who are shooting Malawian citizens in Mangochi Border

 7. Amene akukana ma demo ndi qmene amapitira kuba mma shop so amvetsedwa kuti there will be tight security hense tyis luck of interest.

 8. Achita bwino chifukwa amapita ku nseu ndicholinga choti akabe. Machitsanzo, pa 20 July ana a pa Poly anaphwanya Peopple’s ku Chitawira.

 9. yah we don’t need cowards here that why Malawians are taken for granted why people are fleeing their own country in large numbers. This means poverty is at the worsen point.

 10. Koma nanu Amalawi 24 pena pake sindimakumvetsani ndipo ndinunso oyambanitsa. Apatu nkhani siyokakamizana ndipo ndiufulu wamunthu kupita kapena kusapita. Koma chomwe tingadziwe ndichakuti protest ili mmalamulo Adziko lino ndipo enanu mukungolankhula coz anthu akudziweni kuti mumatukwana. Koma sizoona ndipo sibwino munthu kitchuka ndikunyoza ena, apapa zomwe mukulankhula ndi zolinga za protest zikuchita kuonekelatu palibe chomwe mukuchidziwa

 11. Mukuvutikilanji a Malawi ? palibe emwe akulakwa or kukhoza , Mark my word ” NTHAWI YAMBUYE YAYANDIKA SIVUTO LAMUNTHU ALIYENSE NKHALANI OCHITA MAU” GOD BLESS HIS WORLD …..

 12. Osamawopa iifa Where Is Our Life Presedent? Who Are Them Lisen Music Of Lucius Know As Life Ndalora Mwazi Wanga Kukha Petro Oyendetsra Dzikolino

 13. Gueyz Can U Rembr Tm Of Malemu Bingu We Was Lost alotof Friends $ Relatives Through Viz Way Pitn Maliro Tidzaika Pot Pan Univesty nd Dzn Phind NJee! Dzitsr Nose Ma Politicias Simuganizira Anthu Anu Panyapanu Pamodzi Ndi Pitala Wanuyo Sidakodwe Polemb Koma Chsn Nduchtsr Wanu Patumbo Panu Mangeni Ndife Ngt Matafale Kapena Lobart Chasowa .

 14. Mbuzi inu ana asukulu nonse ndipo musapitedi chifukwa cholinga cha mademo away simukuchidziwa. Ndipo inu ndiamene mumayambisa zipolowe mukapita Ku msewu. Ana asukulu nonse ndinu agalu opanda nzeru, zitsiru nonse. Ngati ukuwerenga message iyi ndiwe mwana wa sukulu udziwe kuti ndiwe galu, mbuzi ndi bulu. Uzakhala wanzelu ukazamaliza sukulu loma panopa ndiwe galu basis, tisiyileni izi Ife anthu okhwima m’maganizo.

 15. Awa amalawi twenty four wa akunama ifeyo monga mafana apa must takonzeka kuyenda wandawalawu ifenso zimatipweteka zachamba basi

 16. Polytechnic and Chanco students are cowards! The reforms are meant to prepare a better future Malawi, for you and your children!!! So you still.want your fathers to fight your war for you? They already fought their war which led to Malawi’s independence whose fruits you are enjoying today. I salute Mzuni students who are couragous enough to participate in the walk. This is also why Malawi is way behind in politics because the youth are very docile, always waiting for others others to do the work for them and yet always complaining that the government is full of old people! Come on University students, participate in these PEACEFUL DEMONSTRATIONS.

 17. Apatu zasonyeza kuti ophunzila ali ndi nzelu pa okha.osamangotengeka ndi zinazilizonse komanso iwo ongoganiza zosokonezawo achita manyazi.inu chinachilichonse mufuna muononge basi kenako mugwilizane amatele?kodi umphawi ungathe tsiku limodzi?ife ndiye okafa pansewo iwo ali makwawo penapake tisadikile mulungu koma tokha.

 18. Wise pipo think about tomorrow, zimenezo ndie mzeru, inu bakonzani tsogolo la ana anu komanso makolo anu, ndale koma after xool

 19. Akukapanga protest koma mnyumba mwao muli fertilizer wa coupon ,ndikanakhala President mkanangoti tikumana kunsewu konko, kkkk kuona m’busa wavala mkanjo koma akuthawa.

 20. Omwe Akonza Ma Demo Sakakhalako Wokamwalira Ndi M’malawi Wojijilika.Ine Total 20 July Ndikukumbukabe.Kapangeni Mademo Mbuli Inu.Ife Tikakambirana Ndi Muthalika Za Magesi

 21. Wawooo!!! Thats True Sizoonana Zimenezo Kuti Anthu Ayende Pasewu Cz Anthu Ambiri Amataya Miyoyo Yawo. Akafuna Apite Okha Omwe Akufuna Kt Ziterowo Km Ife Ayi Ayi Tisafele Zaeni

 22. Wawooo!!! Thats True Sizoonana Zimenezo Kuti Anthu Ayende Pasewu Cz Anthu Ambiri Amataya Miyoyo Yawo. Akafuna Apite Okha Omwe Akufuna Kt Ziterowo Km Ife Ayi Ayi Tisafele Zaeni

 23. These are what we may call the real responsible future leaders Malawi can be proud of. Nthawi yogwiritsidwa ntchito ndi azibambo aulesi inatha. Let them go and march.

 24. After all they are students of corz. …and no need to quit lessons for demos…..Kuli akuluakulu kunjaku ndi ena omwe adaturuka kalekale mma university mo ali kunjaku looking for job opportunities….sidzikuyenda coz of these political thugs who are stealing tax payers ‘money and never want to fulfill their promises…. Justice cannot lose ..It shall prevail and people are hungry for this…..

  This Govt always twists simple issues making them tough to tackle why??
  Let the MPs debate on the ERB and everyone will decide which is which for Malawi to move on….

 25. Kodi anyani mmazimva kuti amabungwe amakutumani mndani??? Mukufuna muonongetse katundu ndikuluzitsa miyoyo anthu osalakwa chifukwa chani??? Mpaka lero phindu LA uchitsiru wanu mmati mademo sumnauone. Dzuka Malawi. Supezamo phindu Malawi amzakowo amatumidwa ndi zitsiru zotchedwa azungu

 26. We have many problems that are affecting us like kuzima zima kwa Magetsi, kubedwa kwa mankhwara nzipatala zanthu za boma, kusowa kwa maphunziro apamwamba, just to mention a few. Nthawi imene kumachita ma demonstrations okhudza Magetsi amipingo sanatenge nawo mbari ndipo kunsewu kunali anthu ochepa kwambiri, koma chonsecho Magetsi ndi engine yoyendera chuma cha dziko, many people in our country depend on electricity almost everybody is affected with kuzima zima kwa Magetsi koma ampingo sanayankhure kalikonse oro kukhudzika kuti mwina atiyankhulire ife amalawi lero pazinthu zosadziwika bwino bwino ngati zimenezi mukufuna muwanamize anthu mudzina la mpingo kuti apite kunsewu? Akanakhara ma demonstrations okhudza kukwiya ndi mabvuto amagetsi ndikanapita nawo koma izi mmmmh pitani nokha.

 27. kma ndikumva chison ndianthu odzitcha opemphelawa mwaiwala kale anthu aja mudawephesa ulele aja tatiuzani ndiphindulanja lomwe lidapezeka paimfa yaanthu osalakwa aja? nanga unoyo amene munatsogolelan mudafa angat ndye wina aziti nyonyonyo ukuti ukumenyela ufulu dzikoli ndilambuyako ok dpp yaketu ndiyomweye ndipo singagonje ndyokonzeka kukamwaza zipolopolo pita pa 14 tikakuika ufela yazii usemphana nayo khisimisi kkkkk kufela dziko zaziii zikapangan kapala kumunda iya iyi nd diphiphi

 28. Leave them they think they’re clever. one day you will need also same pple to fight for your rights. Who are you any way just little flickers whether with or without you we’re still going to demonstrate this is our right

  • Pliz musabe kumudzikoyi kapena kupha anthu fear God nanuso achurch mukusowa zolengeza ku church ,pangani manyazi asiyeni a munthalika alamulile dzikoli nthawi ikadzakwana adzachoka munawavotelatu nokha ndiye osamapanga zau devils ayi ,pliz

 29. mkhani ndiyakuti amene afuna kukapanga mademowo have seen that,their bags are ampty known akufuna kuti akhale ndi ma aloawers oti agulire galimoto.

 30. Koma tikumbutsanepo apa ngati papedzeke oluza moyo kapena kuvulala nonse okhuzidwa kokadandaula chipepeso ndi ku PAC osati ku boma nde tisazamve wina akuti boma silinathandize taneneratu apa

 31. Alibe chikondi. Mmalo motiuza zachipulumutso akumemeza anthu kuti tikapange zinthu zoti tizakhumudwanso. 50 plus 1 ndiyabwino kwambiri koma singapangitse kuti zoko liyendebwino pajatu tiyamba kuvota akawina ndipamene amaonesa khalidwe lake. eg first term ya Bingu anayendesa bwino kwambiri koma mene amkawina koyambakaja anthu ambiri samukonde . Tiyeni tilimbike kupemphe Mlungu amamva simzele, simphamvu koma mpemphero mzotheka

 32. Koma 13december ikuchedwa bwanji,,,ndikufuna ndizamve mene zitazatherere ndizakhala ndikumvera radio the whole day coz ndili ndi baby wang’ono ndie sindingakwanitse kupita koma bolani magetsi asazazime kkk

 33. ha ha ha this cadet 24 you screw me so much imagine now at the age of 14 and 12 someone is in the university they are minors please and they cant make decisions on their own they depend on us to guide them kkkkkkkkk ask me how much they need for pocket money ha ha ha ha gum gum sweets

 34. How many times have you done this animal called demo? What have you achieved besides destroying buildings and losing life! Don’t follow blindly e organisers get allowance from NGOs.Don’t be used to fight useless battles,Wait for the election day.

 35. achita bwino Coz amenewo ndiamene amasokoneza these demos will only need matured people not ana a xool Coz amayambisa kugenda ndikuba katundu waathu

 36. Vutoli need a long solution not going to the road you think it gonna solve it ? No ways let people who knows this staff strategies and work on it not just criticizing , have positive mind contribute to what you think can be done they are proper channels for that , act like patriot.dont just think about yourself think of the future of your children, act like sustainabile Malawian criticism want do us anything let join hand on developing this country that’s the true meaning of democracy..

 37. Timakudziwani kale qt mudazolowera kumanama inu,,,,truth abt the matter is that akufuna awaunikire anthu amipingo yawo details corncening 50+1,,,,osati kutemesa nkhwanga pamwala kapena anabwera kwainu mkuwabwereka nkhwangwayo? komanso even if they will fail to join their fellow demonstrators zilibe ntchito bola 50+1 itheke that’s all.

 38. I doubt if this chikalata has been endorsed by the majority of them. Twalemba ichi twagulidwa ndithu chifukwa ana akuma Universities ndiwo omwe ayenera kumvetsa cholinga cha 50+1 chifukwa ndiwo atsogoleri a mawa! Hmm Chikalatachi ndi Chaboza!!!

 39. Ife monga ana asukulu za ukachenjede tatititsutse ndizomwe zalembedwazi, ife ma demo ndiye kudya kwathu moti tikungoona kuchedwa kut pa 13 pafike, Tili komko wina asakunamidzen

 40. They are just few people, I doubt if they even make two thousand people in all the government universities. In Malawi, there are 16 million people plus.

 41. Ose amatenga mbali pa zionetselo ngati izi ndi mbuli zadziko zosowa chochita ,atsogoleli athuwa ose nganyela mukafufuza bwinobwino mupeza kuti pa zionetselozi wina apasidwapo ya coconut & iwe ozitengelawe zingokupwetekesa mutu,keep it up ana school muzikhala osiyana pakati pa mbuli zadziko ndinu, ulemu wanu mutenge,

 42. They are kids we didn’t even ask for their support ife makolo tiwapangira izi akamaliza Xul adzafikire pa bwino kkkkkk let them be in class

 43. Tikanyowe ndi nvula pansewu ngat chisiru…omwe akulimbikisa ma demo azakhala akumwa coffie kwawo uku akuonera ma filimu pa dstv..ma demo akachitika alandileno ndalama ..nzangawe nkukagonaso ndi njala…bola kumazangozikanda zizandipindulira

 44. Hahahaha ife monga makolo awo tikawaimilila and ubwino wake adzauona patsogolo ifeso tinakhalako ana a school pano ndiife azibambo ozindikila alekeni anawo aphunzile kiti azindikile ngati ifeee kkkkkkkkkkkkk Go konko pa 13

 45. Munayambira kutaya nthawi ndikupanga zionesero muja ndiphindu lanji linaonekapo kuti zinthu zasitha anawa achita bwino coz bora aziwerenga ziwathandiza kaa.

 46. Ine ngati tate, ndikuwona kuti nkhanizi ndi zopusa kwambiri. Kodi dziko lathu lino lili ndi ndalama zomazapangitsa zisankho kambirimbiri ngati mapulezident atapezeka kuti akufanana mavoti? Ndalama zachisankho sizimachokera ku tchalitchi zimachokera mmatumba mwathu, sizampingo. Kodi a mipingo mumadziwa kuwawa kwa Misonkho? Bwanji osalimbana ndi mavuto a magetsi omwe akupangita ophunzira a musukulu zanu kulephera kuwerenga? Ine ndikulephera kuwerenga baibulo chifukwa cha magetsi. Ndiye ndizikavina ku nsewu chifukwa cha 50+1? zopusa

 47. Zoona ndithu, ngakhale Kanyimbi sapita nawo ku nsewuko, Kanyimbi adzakhala ali ku Munda kuthira fetereza. Kodi bwanji amipingo osapempha anthu kuti apempherere dziko lino? Kodi mwafika powona kuti Mulungu wakanika ndiye mulowe mmalo mwake? Kodi zimenezi zikuphunzitsa anthu kukhala odalira pemphero?

  • Komanso a DPP, pena zikudabwitsa.? Kugona kotereku bwanji? Kodi bwanji osaimika nkhani ya misewu, ndalamazo ndikulowetsa ku Magetsi bwanji? So you do not know the differents between needs and wants?

 48. Imeneyo ndiyo DPP yangolemba yonkha chikalata kuvomeleza kuti pa 20 idampha anthu ndi kupatsa chikalatacho kwa ma sapota make mu ma university koma pa 13 Dec tonse tizakhala tasekera school ndipo tikayenda pa mseu ngati nzika yokwuzindwa

%d bloggers like this: