Longezani katundu wanu mu bomamo ndipo yambani kukonzekela ulendo obwelela ku mudzi chifukwa pa chisankho cha 2019 anthu savotelanso a Peter Mutharika ndi chipani chawo cha DPP.
Malinga ndi kafukufuku wa bungwe la African Confidential, ati tsogolo loti a Peter Mutharika ndi kupambana mu chisankho cha 2019 si lowala konse.
Malinga ndi bungweli, chikoka cha a Mutharika chakhala chikuchepa mu zaka zomwe iwo akhala Mtsogoleri wa dziko la Malawi.
A bungweli ati a Malawi akhala okhumudwa ndi kuti a Mutharika akukanika kuonetsa chamuna pa nkhani ya katangale komanso ati iwo akugawa ma udindo mokondela.
Ati angopatsa anthu akwawo basi.
Iwo ati kamba ka izi, anthu ambiri atha osazavotela a Mutharika mu chisankho cha 2019.
Koma mneneri wa boma a Nicholas Dausi ati kafukufuku ameneyu ndi osaona mtima ndinso wa mtopola.
A Dausi ati a Mutharika ayesetsa ku mbali yawo ndipo akhala akugawa ma udindo kwa a Malawi onse mosatengela zigawo.
Poyamba linali bungwe la AFROBARROMETER. Now bungwe la Africa confidential lati Mr. Ibu will be voted out of power. Kodi a dausi mabungwe onsewa ndi onama???? Wakumva amve ndipo ali ndi makutu amvetsetse. Boma libwelera kwawo 2019. amalawi atopa ndi predident osatha kupereka chiganizo zinthu zikakhala kuti siziribwino.
Amenewa ajaila aiwala kuti kadauluka………
Wawoo