A Mutharika alibe chikoka ndipo 2019 sapambana – kafukufuku watelo

Advertisement
Saulos Chilima, Peter Mutharika

Longezani katundu wanu mu bomamo ndipo yambani kukonzekela ulendo obwelela ku mudzi chifukwa pa chisankho cha 2019 anthu savotelanso a Peter Mutharika ndi chipani chawo cha DPP.

Malinga ndi kafukufuku wa bungwe la African Confidential, ati tsogolo loti a Peter Mutharika ndi kupambana mu chisankho cha 2019 si lowala konse.

Saulos Chilima, Peter Mutharika
Chikoka cha a Mutharika chikuchepa.

Malinga ndi bungweli, chikoka cha a Mutharika chakhala chikuchepa mu zaka zomwe iwo akhala Mtsogoleri wa dziko la Malawi.

A bungweli ati a Malawi akhala okhumudwa ndi kuti a Mutharika akukanika kuonetsa chamuna pa nkhani ya katangale komanso ati iwo akugawa ma udindo mokondela.

Ati angopatsa anthu akwawo basi.

Iwo ati kamba ka izi, anthu ambiri atha osazavotela a Mutharika mu chisankho cha 2019.

Koma mneneri wa boma a Nicholas Dausi ati kafukufuku ameneyu ndi osaona mtima ndinso wa mtopola.

A Dausi ati a Mutharika ayesetsa ku mbali yawo ndipo akhala akugawa ma udindo kwa a Malawi onse mosatengela zigawo.