Anthu ogwira ntchito ku mabwalo a milandu m’dziko muno ali pa chiopsezo chosalandira malipiro a mwezi uno ngati sabwelera ku ntchito msanga.
Izi ndi malinga ndikalata yomwe boma latulutsa yomwe yasayinidwa ndi mlembi wamkulu wa boma a Lloyd Muhara.
Boma lati kunyanyala ntchito komwe ogwira ntchito akupanga ndikosaloledwa ndipo ndikolakwia malamulo a dziko lino.
Mukalatayi, boma kudzera kwa a Muhara lati pempho lomwe ogwira ntchito ku mabwalo ozengera milandu akupempha ndilosamveka ndipo lati zomwe akufuna zoti boma liziwalipilira nyumba zawo ndizosatheka kamba poti izi sizinalembedwe mu mgwirizano wawo pomwe amalembedwa ntchito.
Choncho boma lati wina aliyense yemwe akunyanyala ntchito abwerere ku ntchito mwansangansanga ndipo lati yemwe alephere aona chidameta nkhanga mpala.
Mwazina boma lati onse omwe akanatsitsitse mwa ntu wa galu kubwelera ku ntchito, salandira malipiro awo a mwezi uno wa Ogasiti.
“Boma choncho likulamula kuti ogwira ntchito Ku mabwalo a milandu abwelere ku ntchito mwamsangamsanga ndipo onse olephera kutelo achotsedwa.
“Boma silipelekaso malipiro kwaonse omwe akhale akupitilizabe kunyanyala ntchito ndipo boma lichitapo kanthu motsata malamulo pakunyanyalaku,” yatelo mbali ina ya kalatayi.
Kupatula kusalandira ndalama za mwezi uno, ogwira ntchitowa ali pachiopsezo choti mwina atha kuchotsedwa ntchito kamba koti boma lanena kuti ngati anthuwa akanitsitse kubwelera Ku ntchito lipanga zomwe silinanene koma lati lipanga mogwirizana ndi malamulo a ntchito.
Anthuwa alamulidwaso kuti achotse zinthu zonse zomwe aika muzipata zopitila kumabwalo ozengera milandu.