Bambo wa danzi apezeka ataphedwa ndi kudulidwa mutu ku Mulanje

217

Apolisi a mu dziko muno achenjeza a Bambo onse a danzi kuti aziyenda mosamala zitadziwika kuti Bambo wina wa danzi achiwembu amupha ndi kumudula mutu mu boma la Mulanje.

PoliceApolisi ati Bambo wina wa zaka 86 amene anali ndi danzi anapezeka ataphedwa ndi kudulidwa mutu ku Mulanje. Iwo ati anthu achiwembuwo anakamutaya mu chimbuzi atamupha.

Apolisi ati agwila mnyamata wina wa zaka 23 pokhudzana ndi nkhani imeneyi.

“Padakali pano, a Thyolani Khoriwa a zaka 23 atsekeledwa mokhudzana ndi nkhani imeneyi ndipo anzawo ena awiri akufunidwa ndi Apolisi,” mneneri wa Apolisi a James Kadadzera atelo.

Nkhani zopha anthu a danzi zayamba kudziwika kuyambila pamene boma la Mozambique linachenjeza kuti mu dzikomo anthu achiwembu akusaka mitu ya danzi ati ndi chikhulupiriro choti muli golide.

Sabata ziwiri zapitazo, Apolisi ku Mozambique adanena kuti anthu a ku Malawi ndi ku Tanzania ndiwo akutsogolera khalidwe lonunkhali.

Share.

217 Comments

 1. Nothing to say even my cheeks hot tears stop burning me,why?we listen to evil news always.Pple still believe in idols,wealth and famous.Do u think God is sleeping?Do u think God does not see all these things?Do u think u r clever?No u r making a mistake but because we are not belong to this world,I surrender my life for the sake of God.

 2. nchifukwa chiani tsamba lino limakonda kusindikiza nkhani zabodza ife tili ku mulanje komko tatiuza mbali yomwe kwa phedwa munthuyo kt tikaone amalaw nthaw zonse timafuna kunamiza azathu ena omwe ali kutali cholinga chongofuna kuipitsa mbili ya dera

 3. Kwa amene musakukhulupilila khulupililani nkhaniyi ndi yoona ndithu. Ndipo ophedwawo anali amalume anga a mmudzi mwa Makuluni TA Njema mboma la Mulanje. Timawati bambo Khonanga Makwete ndipo anali a dadzi koma okalamba ndithu. Malemuwa amasungidwa ndi ana awo ndipo amagona okha mu kanyumba komwe amagonako. Kucha kwa Monday mnyumba mwawo munapezeka magazi koma iwo munalibemo. Anthu anawafufuza dzuwa lonse koma sanapezeke. Thupi lawo linapezeka Tuesday mu chimbudzi chokumba cha nyuwani pakhomo pa banja lina koma lopanda mutu. A police anatenga amayi a pakhomopo pomwe anawo omwe amatchuka ndi khalidwe lakuba athawa. Mayiwo ndi omwe akuwulula zoti ana awo ndi omwe achita chipongwecho akuti anapeza nsika wa mutu wa dadzi. Tikunena pano mayiawo ali mmanja mwa police ndipo anthu okwiya awotcha nyumba ziwiri za pakhomopo. Chabw a Malawi14 angoyifotokoza mwachidule koma nkhaniyi ndiyoona

 4. Dziko la pasi chop money ndichomcho komaso kumakumbuka tsiku lakutha moyo wako. umadula mzako mutu lelo usanalandile zammanja umazidikila Mulungu kumakuitana smart.

 5. Mutu atenga or angousiya? Ngati atenga mwadziwa bwanji kuti adali ndi danzi or waphedwa chifukwa chakuti adali ndi danzi? Be professional pliz. Dont only be writing things to be famous rather than popular.write something u r sure of. The truth will b known only when the murderer is cought. Osakolezera kupha adanzi pliz.

 6. If stephen aman richly blssd by GOD and full ov power performed great miracles and wonders among the ppl was stoned publicaly by members of the council ,why is it the grvment ,police seeking for aprove by bring murderers b4 court ,they shld stoned publicaly 2

 7. Kenako muyamba kupha onenepa,kenako oonda, kenako oyera, kenako akuda!
  This is bullshit, umphawi unatipweteka. We are only thinking of shortcut ways to get money. Sad

 8. A police mukumalimbana ndi ma min bus driver ndi ovala camouflage za masana izi malo mothana ndi mchitidwe umenewu ntchito yanu ndikuteteza anthu adziko lanu…umuzigwira ntchito usiku oasmangokhala pa office

 9. that’s really a pathetic behaviour. but that’s not the way to prosper in life. no no no…. Malawians calm down. our colonial masters have something to do with this. I will explain. u guess their main agenda is to blindfold us. they want us to stop believing in biblical things. I do bliv that they want to lie to us. they want some pure lunatic educated people to convert us. especially these tumbuka who takes almost 45 yrs doing primary n tertiary education. we all know how stupid they are. but wait. they will use those bones n skulls to provide some cheap n shallow proofs . I don’t care what some dick heads will try to look like they r saints. the truth have been said . all my statements are normative. don’t talk trush

 10. Tawauzani makape apolicewo ndithana nawo akapanda kupeza wapanga zimenezi .. Koma kuba basi.. Infa yamunthu iwowo amafuna ndlama zilowe nthumba bas

  Nanuso mazoba mwaposta nkhaniy ndnu otani? Simunaonepo wadazi ataphedwa?

 11. Eeeeeesh umphawi Ku Malawi unanyanya,zochotsana maliseche ,kupha albino zatha tsopano ?zayamba zamadazi ..bwanji Ku Botswana ,Zambia ,Namibia Kenya ndimaiko ambiri mu Africa sizinachitikepo izi…

 12. Permanent Hair Disaster(PhD) likhalenso vuto lot tizvutika nalo..? plz plz muzimvako chisoni…mwapha albino…sakukukwanani pano mwatembenukila kwa anthu adazi?? mmm almighty God will intervene & bring judgment to all people who indulge themselves in that stupid business.

Leave a Reply