Letsani mitala ndipo pasapezeke obeleka ana oposa awiri – Phungu auza boma

418

Phungu wa dera la kumadzulo mu boma la Nsanje, a Chidanti Malunga auza Boma kuti likhazikitse lamulo loletsa a Malawi kubeleka ana oposa awiri.

dr-joseph-chidanti-malunga

Chidanti Malunga: Anthu asamakhale ndi ana oposa awiri

A Malunga anauza wailesi youlutsa mawu ya boma ya MBC kuti boma likuyenela kuchitapo kanthu kuti achepetse chiwelengelo cha anthu mu dziko muno.

“Anthutu tikuswana ndipo ngati sitichenjela, tikhala pa mavuto adzaoneni,” anatelo a Malunga.

Iwo ananena kuti pofuna kupewa mavuto amene angadze ngati a Malawi angapitilize kuswana ngati ngumbi, Boma likuyenela kukhazikitsa lamulo loletsa anthu kukhala ndi ana ambiri.

“Tikati banja lizikhala ndi mwana m’modzi basi ndiye ilakwa, a Malawi ambiri savomela. Koma tinene awiri, anthu asamakhale ndi ana oposa awiri,” anatelo a Malunga.

Iwo anaonjezelapo kuti Boma lionjezelepo poletsa mitala.

“Mamuna azikhala ndi mkazi m’modzi basi. Osati uku mkazi wina kukabeleka ana kumeneko, uku wina kukabelekako ana,” anatelo a Malunga.

Share.

418 Comments

 1. China did it and it worked for them . Malawi however isn’t ready for such . 2 children maximum would be good. It would make sense economically. Malawi talks of development but she is not ready to pay the price of it.

 2. Iweyo uli ndi ana angati? nanga ku ku zibwenzi zako kuli ana angati onse pamodzi? kapena ukutengera kugwa mpapaya kwakoko eti? mbuzi ya munthu! wasowa mfundo eti, nanga bwanji osangokhala chete, tamuoneni nkhope ngati loweruka.

 3. Akunena zoona cz amalawi umphawi wachuluka xinthu zikusintha daily Mabanja amene sakulimba zikupedzeka kut mai alindiana 5 koma akusamala yekha zosakhala bwino kuzunzisa ana maphunzilo palibe owathandiza ine mfundo imeneyo ndikugwilizana nayo

 4. Kumangokamba Zopusa Basi Anayesanji Anakuvoterawo Munthu Opanda Mfundo Iwe Iwe Pamene Wasiya Kuberekapo Ukufuna Uwakhomerere Amzako Pita Uko Ndimfundo Zako Zopoirazo

 5. Wat i learnt is that in other richer countries the gvt takes action on bearing of kids,which makes anthu have smaller number of kids in their families kut atukule dziko lawo.n if old ones who can’t tukula dzikolo achuluka,families r told by the same gvt to bear mo kids kut ther Should b more energetic young anthu to tukula their country,that’s generations gap.whilst here in maiko osauka yes gvt can say have smaller number of kids,but many times it can’t work cz many anthu av no other things to do than making babies since ther are few jobs n zochitika zna for munthu to be doing n sizikhala zodabwisa to c anthu having more than 3kids in their families.but we really can make a change cz kudalira kwachuluka kwambiri. Its a welcome development.

 6. Fundoyi Ndiyabwino Kwambiri Ngakhale Ena Mukulesa Vuto Mukabeleka Ana Phwi Ngati Ankhanga Njala Ikafika Mumatukana Boma Ndi Mabungwe Kuti Sakuthandizani Ngati Bomalo Ndilomwe Linakutumani Kuti Mubeleke Anawo Ana Ambiri Koma Polima Mulibe Muziwapasa Chani Anawo? Munthu Akazi Atatu No Chochita Zachamba Bas

 7. Bwana mp, msatangwanike ndi zozila,kumbukani mmalawi muno muli mavuto ambili, kusowa kwa mankhwala okwanila,kukwela kwa katundu,kusowa misika ya mbewu,kosowa kwa mijigo,masukulu abwino,miseu ndi zina zotelo.Mr mp simnasakhidwe kukamba za mitala,yomwe inayamba pachiambi aAdam ndi Eva atachimwa.

 8. that’s why Malawi is poor, timasowa zonena zaphindu mmnyumba yamalamulo ana ndiomwe akukanika kutukula dziko? or anthu andalenu mukamaba ndalama zaboma kupepela madazi petupetu ati amthu amzeru chonsecho mmitu mulibe aliyense wake up man, talk of something very concrete

 9. What a rubbish proposal iwe ukuziwa kuti for every 100 children born 70 are girl 30 are boy ukaletsa mitala akazi osala 40 akwatiwa ndindani ? Iwe ndi amene umalimbikitsa same sex marriages eti satanic uzikapangila kunyumba kwako osabweretsa zimenezo Ku nyumba ya yamalamulo.

 10. Choyamba sakudziwa birthrate difference between girls and boys, Chachiwiri awapezere mabanja akazi amene samakwatiwao, Chachitatu iye siamene amadyetsa mwana wachitatu kapena wachifolo mmabanja ayiniakewo

 11. Niopusa….mkesa mukukula mimba nindalama zathu izo mulandira…..nimpando wandale uwo…kalankhulani zanzeru….iwe uli ndi ana angati….ngati ubala kwakuvutani…khalani chete…..mp….opanda fundo….no sence….

 12. APA tikungoyankhula zambiri koma nkhaniyi ndiyofunika kuyiganizira bwino aliyense malingana ndimapezedwe ake u can have ten children koma kulephera kuwasamala sizabwinoso kale ndi pano ndizosiyana, of course primary school ndiyaulele koma pali school fund just imagine upeza mwana walephera kupita Ku school becoz of school fund ndiye atati ayambe kulipira fees zingakhale bwanji? Tiziona mbali zonse zonse APA zinthu zikukwera tsiku ndi tsiku komanso zikusintha tsiku ndi tsiku munthu akhale ndi ana oti akwanitse kuwasamala

 13. Mukutsutsana ndimulungu musatilankhulise pambali.kodi mwazindkilaliti kuti anthufetikufunika tikhaleochepa.pachinachilichonse mulungu alinachondicholinga.kodi ndibwino kumvera munthu kasiyamulungu? Asatipusitse azunguwa chifukwa chaumphawi ikani maso patsogolo osasiya kutamandamulungu

 14. nonse amene mukutsutsa pa nkhani imeneyi mulibe nzeru, atsogoleri ngati amenewa ndiwomwe akufunika kulamulra dziko, muganidzre mene chwelengero chilili panopa and think of where we are going, kod mukuganidza kut umphaw umenewu udzatithera? ma resources amene tlnawo pano ndwochepa kwambri so tyeni mudzngoswana ngat makoswe choncho!

 15. This is absolutely nonsense. Why do you say parliament must approve a death penalty for those who steal government money? You want to tell us that all these problems in our country are coming because people are having more than two children? If a government official steals money from the government, is it because we are having three or four children? Let us look at our economy from the time of Dr Kamuzu Banda up to the present then we can have a better solution, we shall find out that Malawi can depend on its on. Find out the population of Lagos city of Nigeria. Always our leaders just think of punishing Malawians with stupid laws

 16. This Mp wanyasa ndimtima omwe ndithu.
  This fool’s of member of parliament must fall in 2019.
  Iyeyo ndiwaNumber 7 m’banja labambo ndimayi ake.
  He must know God, stop copying everything that fucken white people are doing.
  This rule belongs to your family only.
  Rubish

 17. Did you know that African population is very small compared to all continent and the higher the population the higher the continent is developed?eg Asia /China?

 18. A gogo ako anali ndi 10 square km of land. Koma anabereka ana 10. Mwana aliyense anatenga 1square km. A mayi ako nawo anapasidwa 1square km. Inu munabadwanso 10. A mayi ako anagawa aliyense 0.1 square km. Ndiye iwe ubeleke 10. Kodi anawo azagawana bwanji ka 0.1? Kuganiza ndibwino.

 19. Since r still in financial crisis as a country, i request government to introduce fast fees on primary education and hospitals. Increase fees in secondary as u have done in colleges. Please fasten the national IDs to for easy implementation of these things. It when pple who need 20 children will realise the vital of having two children even one.

 20. l think all of you giving comments here are ignorant and you lack understanding and critical thinking. You need to analyse the statement before you comment to avoid the display of your foolishness and ignorance. Do you really know that the world is changing ? Lack of education is something I think is missing here. I would rather prefer if the government comes up with civic education on this topic so that some of us will be able to understand what the MP is trying to put across rather than giving stupid comments which lack understanding of the topic.

 21. Mbuz ya MP zokamba zinamusowa ngat iye akaz ake anasekesa or iyeyo sabeleka akhale choncho ife ndanyamata aphavu sitinanthe or mwana wake wamkaz tikhonza kumgwila ntchito galu nsena önyela mmadzi iwe ife tinakaswana ufune usafune wamva ukambe zina kaya ana 100 ndi anga bola ndiasamale bac anawo amadya kunyumba kwako usamaletu ndi malakhulidwe ako oyipao chisiru iwe undilakwisa bac

 22. If Malawi palament has one idiot member is this Chidanti Malunga. He is paramount idiot of all idiots in Malawi. Anthu aku Nsanje anabeleka satana in the name of this fucken son. Kuipa nkhope kofanana ndi mtima wake omwe

 23. Mr malunga anthu Malawi sadaphunzire mokwanira mmene angagwiritsire ma natural resources kuti apange cuma koma mosamala cilengedweco inu ndi anzanu mutere mucite kafukufuku 1ikani maphunziro one opindulira Malawi mchichewa adziva mosavuta 2mukhazikitse bungee lomwe lidziphunzitsa amalawi zacuma ndi kayendetsedwe ka bizinesi mchichewa 3english idziphunzitsidwa payokha as communication language China, Russia,India amaphunzitsa nzika zake mziyankhulo zawo koma ndiotukuka cifukwa cigulu cimamva ndikutsata zinthu 4aphunzitsi aphunzitsidwe mwaukadaulo kuti adziphunzitsa masayansi subject practically cifukwa colinga cophunzitsira nkuti akapange apply luso lomwe apeza kutukulira miyoyo yao komaso dziko most Malawian teachers are exam oriented as a result we fail to produce and export.chidant we are now friends.

 24. Ngati mungayambe kuthesa mvuto laufiti kaye ndikhoza kugwirizana nanu. Poti munthu azunguwa akabereka awo awiri palibeso zoti mwina kubwere mfiti kuphera anawo , ndiye Malawi amene ndimaziwa ine azakuphera tomweto tiwirito ndiye mabvuto abale.

 25. Kusakhala Ndi Nzeru Phungu Ameneyo Mmalo Moti Mzikambirana Zothetsa Njala Ndi Umphawi Kumatha Alawansi Ya Boma Kumakambirana Za Mitala. Mwina Shaft Ya Phunguyu Yilibe Mphamvu. Asiyen Akutha Kukhala Ndi Mitala Azitero

 26. Mr mp ngat mwatopa ndikumulelera ana awina wake ingomuuzani zoyeneleka kuchita osat zikhudze gulu.

  Mzovuta wina wake kuti mumuuze pazakuchuluka kwa ana chikhalirenicho thandizo amasaka yekha

  Nkhani ngat zatha zoti mutha kumakambirana ndibwino kumasiyanapo msanga kusiyana ndikutulutsa ma bill okut sangatheke,cos aliyense amapanga maplan ake malingana ndimmene akumzimvera kapena kuganizira as long as he can afford for the basic needs

 27. Bwana MP,, before you speak please understand peoples actions towards what you talk, implementing this law, it will have a positive and a negative impact towards the population and as well a sin against God, I can give you an example of china, the chinese government implemented this law 20 years + ago if am not making mistake and recently they are trying to revisit the law, because most of the children being born are girls, which is out numbering the population of men in china. So the motion in the house of common was that they should kill a girl child just born.

  Bwana,, it is good for we Malawians to remain as we are or try civic education campaigns about the demerits of having a big family towards social, economic and other services.

  I believe in Holy Bible and Qua ran there is no law which says ” you should have two children”,, as both muslims and christian believes that God told Abraham or Ibrahim to make his name father of many nations, it simply tells us to multiply as we can.

  Bwana about your point, many Malawians I dnt think will tolerate it to pass.

 28. Hahaha so shame on u !! Why dont u come with another wise topic, not this one its everyone’s right to be in polgymmy or no as long as he will manage to support them and a number of kids he agrees with the partner not coming With ideology like this, and people never voted for u to come with that nonsense like this, ask government to rescue people from porvety and youth unemployment not that rubbish u talking here

 29. ndkanakondwa kt bill imenei iduse. an2 tikuonjeza, infact, akanat m’modz like CHINA. an2 tikukhala ngat as if we r COMPETETORS kt tikufuna tiwine LOTTERLY.

 30. Malawian reasoning !!” what about if one dies” mmalawi sazantheka. Umphawi basi tizafanawo!! Botswana only 2 million population. Ndalama yawo it’s almost 1 Botswana pullar to 50-60 Malawi kwacha. Malawi population almost 17 million now!!!

 31. That’s very good plan,kuifunira ubwino dzino.Mulungu anati ngati diso likukuchimwitsa ichotse kuti usachimwenso..Mulungu anati berekanani ngati mchenga koma ngati tikulephera kuwasamalirira ndibwino kubereka ochepa.Look Botswana as a country ndiku desert but ndiyochita bwino chifukwa population ndiyochepa.Tonse timadalira boma kuti mmabanja mwathu kuti ziyende,kwenikweni kuno Ku Malawi.pali zitsanzo zambiri zomwe timati boma timaidalira.

 32. Wasowa chonena kape ameneyu,amene Anatilengayo anati Tiberekane tichulukane,iwe ndiye ndindani kuti ukatsutsane naye sample mayankhulidwe ako,komanso Palibe angaletse misala,siinayambe lero

 33. Umatilelera ana ndiwe,pita ukasambire mushire ngati wasowa chonena kudya ndalama ndi zamkutu.amvekele ndikuyimilira anthu amdera langa,bola kuimira makoswe kuti asaswane mnyumba mwako.

 34. People are a source of market for our produce, a source of labour for our production, among others. I think we dont have to blame people for the poverty we are in, blame government for not having good use of the growing population. Such policies are violations of human rights. Atleast try to invest in education for girls

 35. Kkkkkkkk iyi nde timati Fundoless
  Kuli anthu mmanyumbamu akubeleka ana adzigololo mpaka ana 7 wina aliyense bambo wakewake nde ukanene zoletsa mitala kkkkkk zangovutapo panyasaland Lol

 36. Uchitsiru Sudzatha Amalawi. Anthu Osauka Osawa Pogwira Ana 10 Koma Anthu ozindikira Ndi Ochita Bwino Ana Awiri Basi. Kodi Mwana Kut Akule adziimire Payekha Mumaluza Chuma Choluka Bwanji? Ndiye X10, Mukanakhala Ndiawiri Better. Mufufuze China, Israel, America, Egypt Etc Anayamba Kale Iwe Ndiwe Ndani Kt Utsutse
  Awiri Bas Maganizo Abwino Zedi. China Chisatsutseso

 37. Malunga ndi MP opusa kwambiri iye waswaiswa ana Midzi kunsanje kwAkeko ndiye aziwamphwanyila ena ufulu imeneyo ndimbuzi Kwabasi olo boma Litavomeleza ine sindingasiye kubeleka Chifukwa chameneyo anawo amadyesa ndiiyeyo? Mphwala lake ameneyo

 38. Mr MP can you justify this with valid reasons of why this should be happening.

  Increasing in the population is very important Mr mp bcoz its a way of increasing HUMAN RESOURCES in the country which somehow is very important for the development of this country.

  Don’t worry with the increased number of people in this country, I blv you don’t know that God created natural ways of controlling this..

  If you think the increased number of people is the only reason of creating future problems in this country, then mmmmmm I think you have to revisit ur dictionary..

  The problems you and ur fellow MPs are enough to cause hefty or future problems than the number of people amene sanabadwe….

  How can the un born people create problems in the future while they are not yet born.. This is ridiculous…

  You may never know that out of many unborn people, one will be the person to come and rescue this nation.

  Solve the problems within the available population.

  You have to do a critical COST BENEFIT ANALYSIS, Then come back ok

 39. I support him ine i only have two kids(girls) and there is no reason to go beyond that,what for?i will concentrate on the two invest for myself and for them…….. ana ambiri achiyani olo mpaka 4 mmmmmmmmm i dont care about having my name as most do for having boys after all i would be dead and am not sure what becomes after,as long as i grow my daughters in good spirit education and run business i would die a happy father period…no reason to chase for a boy child and in the end have 6 kids kkkkk

 40. Aphungu anthu mwatibweresera ufiti woopya muno chfkwa cha zokagula na Zanu zoti ufiti kulibe. Nde lero mkuona anthu abereke ana awiri nde fiti ziwatafune. Anthu andalenu ndamene mkutembelera Amalawi Kukhala pa malawi amoto

 41. pepi mr mp ngati mukuona kuti zikolathu tachulukana kulibwino muuze a p m f kuti akuombeleni ma mp nose kuti tichepeko koma osatiphela ufulu anafe ngati ndi satanik mualuka

 42. ameneyu. ndamene akulankhula zanzeru,, caz kumalawi kuno anthu tikuberekana kwambiri,, as aresult ana chitsamaliro chimachepa, @ pano dziko linasintha kubereka ana ambiri zichepe,

 43. School ku primary yaulere,zipatala zaulere,nthawi zina zikativuta ma bungwe komanso maiko akunja amatipatsa chakudya chaulere ndiye mpovuta kwambiri kuona ubwino okhala ndi ana ochepa ndipo zizatitengela nthawi kuti tizasinthe kuteleku wina akumutukwana munthu woti apeleka maganizo abwino koma nayenso achepetsa bolani anakakhala 4 kkkkkkk.

 44. Wachita Chita nao azimai wakwana nao nde uletse anzako!!!!! Anthu amvekere phungu wathu ameneyo kutiimirira, abale nde bolanso wa chamba ujatu, koma uyuyu mbola basi

 45. How many children does he have? We have never ever even visited his home to ask for a help for our children. Stupid. coming 2019 he will need many voters. stupid again. You also have out side children I know

 46. Akadati boma ikupeleka chithandizo monga ndalama every month kwa ana ngati maiko ena tikadati mzotheka. Akulu amenewa ndi amisala asowa chonena ndi ana angati amene iye chiloweren m’boma athandiza ku dera la kwawo?

 47. Ine ndili ndi ana akadzi okhaokha awiri nde uziti ndilekeze pompa tsopano akadziwa aziwateteza ndani? Ndikuyenela kuyesanso mpaka ndipeze wammuna zimenezi zichepe mmalo Malawi muno ndi ambiri tibelekane Basi tizaze zimenezi osazakambanso takana kkkkkkk

  • I support him ine i only have two kids(girls) and there is no reason to go beyond that,what for?i will concentrate on the two invest for myself and for them…….. ana ambiri achiyani olo mpaka 4 mmmmmmmmm i dont care about having my name as most do for having boys after all i would be dead and am not sure what becomes after,as long as i grow my daughters in good spirit education and run business i would die a happy father period…no reason to chase for a boy child and in the end have 6 kids kkkkk

 48. Aphungu ndiwo amatiyimilila ife kunyumba ya malamulo ndipo amati amakamba zomwe tawatuma.

  Mtakufumsani bwana …. Kodi zimenezi ndizomwe akutumani bwana ku dela lanuko? Tiziti kumeneku misewu iliko yokwanila? Ana asukulu akumwa phala mammawa?

  Zoti amzanu mtukula pakhomo anawapondereza kudera kwanuko mukudziwa?

 49. iyeyo ndiwachingati pobadwa, enafe ndi a number 9 zikanakhala zimenezo enafe sitikanabadwa akapange lamulo limenelo mnyumba mwake sizophwanyilana ufulu obeleka ndikubadwa masiku ano,olo ubeleke ana 50 bola ukuwasamalila basi.

 50. Bolako uyu amayankhula koma MP wakwathu chimusankhireni sanayankhulepo ku Parliament amangopita kukamwako tea nkulandira ma allowance nkumabwerako. Ngakhale ka point of order kapena kutsokomola ayi ndithu. Akafuna kutsokomola amatuluka panja akuti mantha. Nthawi yakwana ma MP athu ayambe kumayankhula chichewa mwina wathuyi nkumvekako mawu.

 51. mp ameneyo zomwe akukamba akukhala ngati mutu sukuyenda bwino,kuno kuminzi tiliko anthu ambiri ophunzira koma tikamafunsa ntchito amatenga abale awo ndiye mutititanipo ife,iwesungatipangale ma budget munyumbazanthu ngatitafuna kukhala ndi ana 5tinkhala nawowamva.

 52. Ndetu ku breaker record ya ma mp opanda fundo ndi nzeru zomwe mp ameneyu…ukaletse anthu kubelekana anawo amazadya kunyumba kwanu… Malamulo amenewo uziwuzana iweyo Nda akazi ako ndi Ana ako..chifukwa ndamene amadya zathumba mwako…. Ma rubbish

 53. Even utabereka ana ambiri koma kufa kulibe ixo coz onse akhoza kumwalira nkukhalanso opanda ana ndechongofunika nkuunika bwinobwino mlingo Wa ana omwe banja liyenera kukhala nawo basi. Mundikhululukire ngati penapake ndalemba mosakhala bwino

 54. fodyayu kumazimitsirako..
  vuto siiweyo koma komwe ukuchokera.
  siumadziwa kuti ndi plan ya zibambo aliyese kupanga chisankho?
  kapena ukufuna unene kuti Boma lidzika likupelekaso thandizo kwa mabanjawo?

  kweni kweni ukufuna utiuze kuti chani?

 55. Kuletsa kwabwino mulimbiktse sukulu …chifukwa mwana pomamaliza ku college, amatanganidwa ndi zina osati zopanga ana …zoika lamulo ndizokomela ochepa …Osaiwala bwana malunga paja timabeleka ambili kuti adzatigwile pankono.

 56. Mzeru zopusa kwambiri,anawo ndiako ndpo uziwadyesa ndiiweyo? Wandikwiisa kwabasi ukanakhala pafupi nkadakukhadzula khazula, usamale nd pakamwa pako ponunkhapo

 57. u r ryt Mr mp, muona chitsiru China chitukwana popano apa Kkkkkkkkk ,kwathu kuno zikuonjeza heavy kumwera paka ana full lineup ya flames koma akut ndiamunthu modzi kkkkkkkkk

 58. Do not bring dictatorship into the country. If one has resources and able to support three children or more let them bear more. But for those who can’t afford to support themselves let alone their children maybe its applicable to have two as maximum number. But just don’t dictate about two. My opinion

 59. Ine Ndi Wanumber 4 Kubadwa M’banja Mwathu… Ndiye Makolo Anga Adakati Atsatile Njira Imeneyi Kalelo Sibwenzi Ine Ndilipo! So In Short I Can Say That, I Cant Support That! Its Foolish Decision And Even Bible Says “mubelekane Ngat Mchenga”…. So Who Am I Amene Ndingasinthe Chikonzelo Chamulungu? Ndikabeleka Ana Ambiri Ndidziwadyetsa Ndekha! Ndilibe Problom Ine

 60. Ndiwe wautsiru etiiiii?If you said 4 maximum I would agree with you, but imagine you got one child and that child die while already over the age that you can’t make any child what will you do? Who will enherit your worthy or what you have? Think b4 you bring this to publish

 61. NGATI ANASIYA KUCHINDA NDIZAKE ANAWO AZIWADYESA NDI IYEYO?…IYEYO ALINDI ANA ANGATI? NANGA KWAO KUNABADWA ANA ANGATI?…MUMUWUZE IFE SITILORA…MULUNGU ANATI TICHULUKANE NGATI MCHENGA

Leave a Reply