Mabuluku ong’ambang’amba avuta pa Malawi

Advertisement

Siumphawi koma kufuna kuyenda ndi nthawi kwapangisa achinyamata mu dziko la Malawi kugwa m’chikondi ndi mabuluku ong’ambang’amba.

Mabulukuwa akumakonzedwa m’mawondo ndi mu ntchafu, kupangisa kuti khungu lizionekera kudzera m’mabowo munthu akavala. Kukula kwa mabowowa kukumasiyana.

Kafukufuku waonesa kuti khalidwe limeneli likufalisidwa ndi akatswiri otchuka kumbali ya msangaluso. Monga oyimba, akumakonda kuvala mabuluku okhetekawa mu ma kanema a nyimbo zawo. Ndiye achinyamata owakonda akutengera kuti nawo awoneke otsogola.

Avuta pa Malawi.

Izi sizikutengera kuti ndi nyengo yozizira, pamene achinyamata akumkeramkera namatchena zovala zoterezi. Iwowa akulolera kuti azizidwe bola aoneke mopereka chikoka ndi kuyamikiridwa kuti ndi ozitsata.

Mtundu wamavalidwe amenenewa unafika ndi pakanthawi koma panopa wafikapo. Potengera kuti ku mayiko ena mabuluku wa anakhazikisa maziko pakale, zapangitsa ena kuti anene zoti “zikubwera mochedwa.”

Ngakhale achinyamata agwa m’chikondi ndi mavalidwewa, izi sizili choncho ndi achikulire amene adandaula kuti izi zikuononga chikhalidwe cha a Malawi.

Ngakhale achikulire ena akumazilimbitsa mtima ndi mawu oti “wakalamba wafuna” kenaka nawo nkuvala mabuluku a mtunduwu. Kwa ena opanda makobili okwanira, akumang’amba okha mabulukuwa.

Ogulitsa malonda akupha makwacha koopsa ndi mtundu wazovala umenewu. Posatengera kuti mabulukuwa akumakhala ong’ambang’amba, anthu akumafapo makobiri ankhaninkhani kuti agule.

Ngakhale izi zili chonchi, mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, akulimbikitsa a Malawi kuti azigula zovala zachikhalidwe zosokedwa Ku Malawi konkuno.

Advertisement

263 Comments

  1. Vuto simabulukuwo air.zimene zikuoneka APA anthu anayenera kuonetsa chimene chili mkati anayenera kutero basi.atapanda kutero adzavala ndani zopusazo.

  2. Mudziko la malawi??? Mayiko ambiri inu Malawi24, munthu sangamavale “Nyanda” lero lino, fashion imasintha mosogozana ndi generation imene mulimo, kale anthu amavala mikhajo ma gulu achina yonah,noah yesu,,,ndani ndani,,,chikhala ngati analipo mpaka lero lino bwenzi iwonso akuvala ma buluku,ma suit ma jeanz zonse kutengera m’bado womwe alimowo,,ndiye si malawi yekha yemwe anthu akumvala zong’ambika za new-one,mwinanso malawi nkukhala womaliza pa nkhani ngati zimenezi

  3. Kunena zoona munthu opusa samagwirizana ndi chiphuzitso chabwino taonani enanu mukutukwana coz ndizovala zanu zimenezo km ngakhale mutukwane a 24 akunena zoona nose ovala chonchi ndiopusa .

  4. Plz God av mercy open our spiritual eyez so that we can recognise that we ar in last dayz and satan iz usng anythn kt athe kuwina miyoyo yochuluka (hoseya 4v6)

  5. Hey am from Zimbabwe,,, we are nolonger living in the past,, world over thats the way we dress,,, thats why many African countries fails to success,,,because of background minded,, thumbs to these who wear this clothes thats the fashion

  6. This is an international outfit sikut nd malaw yekha ayi it is the whole world youths are putting on this kind of owsome fassion watchout i gonna show u mine,,,,,lol

  7. Kalekale dzinalikonso koma kungoti those days ukavala anthu ankakumvera chisoni pot udali umphawi lero ukaponyeza nkuika pa FB anthu akumakuyamikira kut watchena even ma flat cap adaliponso kalero koma those days ankavalidwa ndi nkalamba lero ma yo mitchana yasandisa swaga pompano nsapato za splastic zomwe zinkakucheka ukavalazija zibwereranso mu fasho makabudula amabhankolo aja muwaona mayo pompano akutchenera mitchana mumatiimirira

  8. Kalekale dzinalikonso koma kungoti those days ukavala anthu ankakumvera chisoni pot udali umphawi lero ukaponyeza nkuika pa FB anthu akumakuyamikira kut watchena even ma flat cap adaliponso kalero koma those days ankavalidwa ndi nkalamba lero ma yo mitchana yasandisa swaga pompano nsapato za splastic zomwe zinkakucheka ukavalazija zibwereranso mu fasho makabudula amabhankolo aja muwaona mayo pompano akutchenera mitchana mumatiimirira

  9. I don’t understand…Z it a Case…everybody in every Country can wear it…Mukutitayisa nthawi tu,tazinenani nkhani zeni zeni

  10. Historically and culturally Malawi has been showing good example in as far as dressing is concerned. Being a youth, peer pleasure and foreign cultures, social networks_internet inclusive, are among factors diverting our fellow youths to be dressing differently. Though time change is being considered as a contributing factor to their strange dressing, lets emphasize here that, internet, foreign cultures and peer pleasure spoil our youths. However, i dont suggest that we can change the situation. Currently numerous youths are disobidient, decisive, mischief, arrogant. Even if being told to stop doing what is considered bad by their parents, they seldom listen to. As it was written and prophised already, let it happen, let it get established, installed. To those parents who can manage to eradicate this tendancy please help. To those religions which can bring changes, lets hold hands. To those medias which have got potential and strong muscle to bring to an end this negative dressing lets unite.

    1. Kendric Trevor, pliz l may offend u but frankly speaking what the guy wrote is a fact, no matter what. U can bring ur arguments here but this is the point! Where is the world heading to? Read the bible u will realize later

    2. We ain’t English, we are proud of our mother tongue. Visit Tanzania, China, Senegal, Cameroon the list is endless. Be proud of ur culture

  11. The problem is that most people dress like that ignorantly. Dressing acts like a mirror of one’s personality. It also shows lack of taste coupled with indiscipline. Its got nothing to do with riches coz I have seen people who come from rich families dressing decently when they go partying.

  12. Uku ndiye kudziwa kudya kwa ndalama kwa tsopano olo mwana wa president amvala zimennezi kutsonyinza ndalama inu mulibe ndalama ndi amene mukuvala zachikhale .izi zikuchithika mmaiko ambiri onsti kuno konka j

  13. Zubwera mochedwa,pajatu zumayambira mu #America kenako #Africa nkumatengera.anzathu amavala zong’amba Chifukwa zovala zawachulukira,pomwe enafe tili ndi chimodzi chomwecho koma kutengeka

  14. Go to hell … Osamangovala zibiya bwanji azigogo anthu amkavala nyanda iwe umavala? Expect more than this bra its new generation

  15. Zikuchitika evrywhr and dt’s part of life and zinayamba kale kale nthing new about it.unless mwakulila kumizi am shur u dnt knw anythng about fashion.paja muchichewa thers a saying Kuyenda ndikuvina.dnt stick in one plays yendan mayiko ena thn muyiziwa life.

  16. Ndiwe opusa Admin, do u mean it is the first time this type of clothes to b seen in malawi? We r indeed poorest nation on earth if it is like that.

  17. For God sake, that’s fashion!!! Its skinny mukhoza kuvala in winter as well. President pitala akumavala ma suit amu D&G. Let people grab what they love!!!!!

  18. Zotengera, zitipha ndalama mulibe;,,mavuto ali mbwee! Mukumagula zong’ambikazo dala kaya zako izo mphawi mzangawe”””””

  19. Time and internet are biggest contributing factors, there’s nothing anyone can do but let it roll and in due course you will see it fade like it did with all fashion trends before it

  20. MUNTHAWI YOMALIZA ANTHU ADZAVALA NGATI WA MISALA NANGA PAMENEPA MUNGASIYANITSE WA MISALA NDI MUNTHU WABWINO?? MPHAMVU YA DZIWANDA.

    1. aaa hahaha palibe chiwanda chilichose pamenepo akulu….. if you old fashioned basi kukhala chete nd new school imeneo. dirty for life

    2. TIDZAKHALA CHETE MPAKA LITI POMWE DZIKO LIKUPITA KU CHIWONONGEKO? NGATI TIKULANDILA ZILANGO PADZIKO LA PASI NYANSI ZAKE NDI ZIMENEZI NANGA PAMENEPO NDI WAMISALA AKUSIYANA PATI?? SO STUPID.

    1. kkkkkkk! Nchifukwa a Chingambwe FC ikumapha anthu ku stadium chifukwa chifukwa chofuna kumawina ma game,eishiiii! Chi-team chokhwima chomvetsa manyazi ichi.

  21. I was sitting in church and the guy in front of me lit a cigarette, right inside the Church! I was shocked, I almost dropped my beer!

  22. Dziwani kuti dziko LA Malawi ndi kotentha
    Achinyata apezelapo mwayi. KUTI
    Nalo phuthi lipiteko mphepo
    Kkkklkl.

Comments are closed.