Mabuluku ong’ambang’amba avuta pa Malawi

Advertisement

Siumphawi koma kufuna kuyenda ndi nthawi kwapangisa achinyamata mu dziko la Malawi kugwa m’chikondi ndi mabuluku ong’ambang’amba.

Mabulukuwa akumakonzedwa m’mawondo ndi mu ntchafu, kupangisa kuti khungu lizionekera kudzera m’mabowo munthu akavala. Kukula kwa mabowowa kukumasiyana.

Kafukufuku waonesa kuti khalidwe limeneli likufalisidwa ndi akatswiri otchuka kumbali ya msangaluso. Monga oyimba, akumakonda kuvala mabuluku okhetekawa mu ma kanema a nyimbo zawo. Ndiye achinyamata owakonda akutengera kuti nawo awoneke otsogola.

Avuta pa Malawi.

Izi sizikutengera kuti ndi nyengo yozizira, pamene achinyamata akumkeramkera namatchena zovala zoterezi. Iwowa akulolera kuti azizidwe bola aoneke mopereka chikoka ndi kuyamikiridwa kuti ndi ozitsata.

Mtundu wamavalidwe amenenewa unafika ndi pakanthawi koma panopa wafikapo. Potengera kuti ku mayiko ena mabuluku wa anakhazikisa maziko pakale, zapangitsa ena kuti anene zoti “zikubwera mochedwa.”

Ngakhale achinyamata agwa m’chikondi ndi mavalidwewa, izi sizili choncho ndi achikulire amene adandaula kuti izi zikuononga chikhalidwe cha a Malawi.

Ngakhale achikulire ena akumazilimbitsa mtima ndi mawu oti “wakalamba wafuna” kenaka nawo nkuvala mabuluku a mtunduwu. Kwa ena opanda makobili okwanira, akumang’amba okha mabulukuwa.

Ogulitsa malonda akupha makwacha koopsa ndi mtundu wazovala umenewu. Posatengera kuti mabulukuwa akumakhala ong’ambang’amba, anthu akumafapo makobiri ankhaninkhani kuti agule.

Ngakhale izi zili chonchi, mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, akulimbikitsa a Malawi kuti azigula zovala zachikhalidwe zosokedwa Ku Malawi konkuno.