Bambo wa zaka 24 zakubadwa adapezeka atamwalira m’nyumba mwake m’mawa wa la Mulungu mu tauni ya Limbe ku Blantyre.
Potsimikiza za nkhaniyi, wachiwiri kwa m’neneri wa polisi Ku Limbe Widson Nhlane anauza wolemba nkhani wathu kuti bamboyu dzina lake ndi Humphrey Chiwaya ndipo amakhala yekha pa nyumba in pa malaini a railways.
“Malemuyu amakhala yekha komanso anali oledzera mowa kwambiri. Patsikuli anthu okhala nyumba zozungulila sanamuone atatuluka mnyumba chichereni,” anatero m’neneriyu.
Kenako anthu aja anaganiza zomuyang’ana m’nyumba yake ndicholinga kuti atsimikize ngati anali momwemo kapena ayi.
Atafika panyumbapo anaona kuti chitseko chinali chotsekedwa, koma anachikankha mwamphamvu ndikutsekula.
Anthuwa atalowa m’nyumbayi adali odabwa ataona bamboyo ali pakama yake kuoneka kuti watsamira nkono.
Apolisi atatulikira pamalopo anatengera thupi la bamboyo ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth Central mu mzinda ku Blantyre kuti amupime chomwe chidamupha.
Humphrey Chiwaya amachokera m’mudzi wa Lupanga, m’dera la mfumu yaikulu Nsamala Ku Balaka.
Honest reporting as a deterrent to others
sono wamupha nd mowa kapena chan?RIP
Nkhanizi mumazilemba bwanji? Ife tafunsa zimene amapanga? Nanga inuyo mumapanga chani? You shown you’re wickness
RIP madala.
ukuti nthano kapena news we osalemba yako bwanji anthu awelengeko? Rest in peace
Thano kapena nyuzi?
Thano kapena nyuzi?
A Malawi 24 ndichifukwa chani tikatsekula ma link anu timapeza zithuzi ndi ma films olaula?mukuipitsa dzina la Malawi nkhanizi timawelenga siamalalawi okha anthu amaiko enanso amawelenga.Nde musinthe zina mukhale Zolaula24 osaipitsa Malawi ayi
Umasegula link yolakwika bwanawe pepa ndithu
Sudziwa kuti sudziwa
Edson sukunamadi zithuz zimaoneka mmwammba
Ause muntendele
midori in action
Rip
Koma zimangovuta ndimaona ngati ndibwino nthawi zina kumakhala ndikadzukulu kamodzi kupangira ximenexi RIP