Bambo apezeka atamwalira

15

Bambo wa zaka 24 zakubadwa adapezeka atamwalira m’nyumba mwake m’mawa wa la Mulungu mu tauni ya Limbe ku Blantyre.

Potsimikiza za nkhaniyi, wachiwiri kwa m’neneri wa polisi Ku Limbe Widson Nhlane anauza wolemba nkhani wathu kuti bamboyu dzina lake ndi Humphrey Chiwaya ndipo amakhala yekha pa nyumba in pa malaini a railways.

“Malemuyu amakhala yekha komanso anali oledzera mowa kwambiri. Patsikuli anthu okhala nyumba zozungulila sanamuone atatuluka mnyumba chichereni,” anatero m’neneriyu.

Kenako anthu aja anaganiza zomuyang’ana m’nyumba yake ndicholinga kuti atsimikize ngati anali momwemo kapena ayi.

Atafika panyumbapo anaona kuti chitseko chinali chotsekedwa, koma anachikankha mwamphamvu ndikutsekula.

Anthuwa atalowa m’nyumbayi adali odabwa ataona bamboyo ali pakama yake kuoneka kuti watsamira nkono.

Apolisi atatulikira pamalopo anatengera thupi la bamboyo ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth Central mu mzinda ku Blantyre kuti amupime chomwe chidamupha.

Humphrey Chiwaya amachokera m’mudzi wa Lupanga, m’dera la mfumu yaikulu Nsamala Ku Balaka.

Share.

15 Comments

  1. A Malawi 24 ndichifukwa chani tikatsekula ma link anu timapeza zithuzi ndi ma films olaula?mukuipitsa dzina la Malawi nkhanizi timawelenga siamalalawi okha anthu amaiko enanso amawelenga.Nde musinthe zina mukhale Zolaula24 osaipitsa Malawi ayi

%d bloggers like this: