By June 19, 2017

Munkhani yovetsa chisoni, akuba sabata yatha m’boma la Mchinji anafukula manda ndikudula zikope komaso sidze za mtembo.

Malingana ndi malipoti a polisi, nkhaniyi inachitika mmudzi mwa Kadula Malambo mfumu yaikulu Mlonyeni m’bomalo ndipo anthu akuganizila kuti izi zinachitika usiku wa la chinayi pa June 14.

A polisi ati manda omwe anafukulidwawo ndi a Dalitso Zulu wa mmudzi momwemo yemwe anatisiya pa 11 June ndipo mtembo wake unaikidwa mmanda pa 12 lomwe linali tsiku lotsatila.

Chomwe chinatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga mchakuti anthu ena omwe amadutsa munjira yomwe inalambalala mandawa anagwidwa ndimantha othetsa mankhalu ataona manda a malemu Zulu ali ofukulidwa.

Podziwa kuti mutu umodzi suseza denga, anthuwa anakauza zamalodzawa anthu ena omweso anakabenthulira za nkhaniyi amfumu ammudzimo omwe ose anatengana kukaona za malodzazo.

Atafika kumandako kunali mfuu yakulira kwa azibale komaso amzake a malemoyo ataona kuti mandawo analifi ofukulidwa ndipo aliyese anali wachisoni ndipo anakumbuka padzana ali limodzi ndimalemuwo poti panali patangotha masiku awiri chimwalilireni.

Mfumu yammudziyi nayoso inagwidwa ndichisoni ndipo anali kakasi kusowa chochita koma akulu ndi mdambo mothera moto ndipo anakaisiya nkhaniyi kupolisi.

Mosazengereza apolisiwa anafika pamalopa ndipo anautengera mtembowo Ku chipatala cha chikulu m’bomali komwe anakauyeza.

Zotsatira zakuvhipatalaku zinaonetsa kuti ziwalo zina pa mtembowo zinali zitadulidwa ndichipangizo chakuthwa kwambiri chomwe akuchipatalawo akuganizira kuti ndi lezala.

Achipatala atsimikiza kuti anthu omwe anachita izi anadula zikope zonse komaso sidze pa thupili.

Padakali pano, apolisi ati akhazikitsa kafukufuku Lusaka zifwamba zomwe zinavhita zachipongwezi ndipo ati Ali ndivhikhulupiliro kuti zifwambazi zigwidwa posachedwapa.

Aka sikoyamba kuti zinthu zamtundu uwu zichitike mdziko muno koma kwambiri zimachitika kwa anthu omwe anatisiya a mtundu was chialubino.
76 Comments

 1. Sibo anthunu lekani idzi

 2. Yona Jausi says:

  Malawi need prayers

 3. Vutoso lina,zakumidima ndi za satana ndiye enafe tikangoti ndiafiti ameneo a malawi 24 mkuti kulibe afiti ku malawi nanga ziwalo zadulidwazo?

 4. Ayi ndithu matsiku otsiriza ano tizimveramvera

 5. Sangalalani padziko lapansi pano ndiziwalo zawanthu mukugulisazo, mukaziona mukamwalira,

 6. Amos Kufa says:

  Zakhala bwino tadziwa kut tisamavutikeso ndikukumba manda tizingoika kunyumba kwao.

 7. Amenewo si akuba koma mukanati..Ziwanda za anthu zafukula manda

 8. Kulemera niggaz size ya Hood

 9. Koma abale kumwamba kuli moto ndinthu pano anthu anasiya kuopa mulungu koma ndalama ndimene ili pa tsogolo shaaaa mudzakayakha patsiku lachiweluzo

 10. Helen Musa says:

  Ambuye chilitsani dziko lathu

 11. inuyo aboma ndizimene mukufuna
  Vuto anthu otelowo akagwidwa mukumachaja ndalama mukuganiza kuti angasinthe chifukwa chowalipilisa ndalama.

 12. shaaa!koma inu,bolaniko zikoli mulungu alinyenyenyenye ndikuliotcha bc tikhale opanda thiscountry

 13. Yousuf Wanena Asowa Tchito Apolisiwo Akazipeza Kuti Mfitizo Mmesa Niomweo Amat There Is No Witchs Here In MALAWI zankutu!

 14. Sue Chioza says:

  Sichinatu? Koma umbuli ndi umphawi…mkutheka alipo wa pusisa..asing’angawa

 15. 4 What Msidze Ndi Zikopezo?

 16. Koma nkhungu lamuthu wachikuda silizava iyayi

 17. Bodza Inu Dzikafukulan Mutileke Ife Alobino Mwina Tiwupezeko akufawo Alibe Tchito.

 18. Musaiware kuti diso LA Jehovah likuona ..mudza lasidwa ndi mpeni okutwa konse konse,inu mwapanga zimenezi

 19. koma zoopsya ndithu eeeeee eeeeee nmalawi ndi moto ovuta kuuuzimitsa npaka malilo kukafukula mmmm mmmm dziweni yesu makosana

 20. Malawi wa lero ameneyo

 21. Zikucika ngakhale mwathu muno anthu amagulitsanso bokosi atafukula.

 22. iiiiiiii am shocked guys

 23. Akut Ndalama Zili Pa Minga Ndie Eeeee Kuvuta Hvy

 24. Malawi walero,ndichani?,kenako tiyamba kudula ana anthu omwe atatione ndani.

 25. Eish abale inu… mpaka maliro? Ngakhale kutembeleledwako mmm this too much now….. mkulimba mtima kwanji kumakafukula mtembo?

 26. Ndalamazi Zitionesa Dzithu

 27. Awa siakuba koma afiti

 28. Sky Nkhoma says:

  Mwasiyanso adazi aja mwayamba kuthana ndi sidze kkk.imeneyinso ndi dilu eti?

 29. Mwikho,maluzi omwewa ?

 30. Achita bwino ntchito zikusowa mwina nkumagwirako zomwezo iyaa

 31. Aba sidze ndi dzikope dza munthu wakufa? Alakwa.

 32. Eish! koma dzikoli likupita kuti? nanga lili kuti lili kuti a nzanga dziko lija romwe ana tinkatsekeledwa mnyumba kukachitika maliro……so sad and shame yooooooh!

 33. Anawawona ndani? Malawi bodza

 34. Kupusa Kumeneko.
  Kusowa Zochita Bax

 35. Kodi akuti Chimanga K40, Soya K130, Sawa K280 Per kg. Anthu Mkuleka kumakafukura kumanda??? zaulendo uno, zina ukava kamba anga mwara.

 36. Dziko ndi anthu ake, zosausa

 37. bwanj tloreze angoliwotcha dzkol mukuwona bwanj

 38. Duu I think they are Holders of Bachelor Degree in Thefty and Engineering system. And advance certificate in Exhuming system.

 39. Masiku Otsiriza Anthu Adzakhala Okonda Chuma…2 Timoteo 3v1-5.Musadabwe Izi Ndi Zizindikiro Za Nthawi.

 40. oziwa kusakandalama salabada pena paliponse amaponda, bola asakugwire

 41. Joe Pasi says:

  Pepani, koma apolisi apula kanthu pamenepa?#zamtsenga!

 42. too bad,koma sidze abale ndichani??

 43. somethings are difficult to undrsnd… if its as aresult of poverty then its jst too much,

 44. Vic Eneya says:

  Koma ndalamazi zitionetsa zakuda mpaka kufukula mtembo.Ambuye pangani chotheka zafika pena ayi.

 45. Kkkkkkk iiiiii mbanvazi nde zakwiya bad,nsika wa zimenez awupeza kuuti?

Leave a Comment