Khalidwe la a Malawi ndilowola – Mutharika

Advertisement
Peter Mutharika

Lolemba, mtsogoleri wa dziko lino, Pulofesa Peter Mutharika,    anasambwaza a Malawi. Iye anati ndi okhumudwa ndi anthu a dziko lino kamba koti ali ndikhalidwe lonunkha.

Peter Mutharika
A Mutharika athila a Malawi mphepo.

A Mutharika anakamba izi pamene anali pankumano ku Mangochi ndi atsogoleri a zipembedzo zosiyanasiyana ku m’mawa kwa dziko lino.

Pulofesa Mutharika anamema atsogoleriwo kuti ayikize a Malawi m’manja mwa Chisumphi kuti chikhalidwe choipacho chiapitilire.

“Anthu amakhala akutanganidwa ndikufunira anzawo zoipa. Ena akunena kuti dziko lino likunka kuphompho chifukwa cha utsogoleri wanga. Ili ndi bodza chifukwa boma langa lachita zinthu zina zopambana zomwe maboma apitawa analephera kuchita,” anasindika motero.

Mtsogoleri wa asilamu mu dziko lino, Shehe Dinala Chabulika, anapereka mangolomera kwa Mutharika kuti asatekeseke ndimanong’onong’o koma alimbike kutukula dziko lino.

Advertisement

8 Comments

 1. chi bwampini tachiwoneni kuthimbilira ati president za uchitsitur basi!!!!!!!!!!!!!!

 2. Peter mutharika ndigalu wa chabechabe ndipo alibe ulemu,iyeyo akuti amalawi kutanthauza kuti chani nde kuti iyeyo simzika ya Malawi chifukwa ngati ali mzika ya chimalawi ndekuti akutanthauza kuti kuyambila abambo awo amayi awo akazi awo ana awo komanso ndi azibale ake onse ndi wonunkha,Nkkuluyu ndimamtenga ngati wa ulemu komanso ofatsa mwina atisunga,Iyeyo mmalo moti aziyankhula za chitukuko cha dziko akuzalimbana ndi anthu kwanyoza iwalira kuti amalawi omwewo ndi amene anawasankha I wowo kuti ayimile dziko,Ine ndikhulupilira kuti Mr mutharika ine anaphunzira komano kasogoleledwe ka dziko sanaphunzile chifukwa nsogoleri wa dziko sakwiya moti mpaka kumawatukwana anthu ake,Izi zikuonesela poyelayela kuti achikulilewa amafuna kukhala msogoleli osati wa anthu ayi koma ongotidyera ife amalawi ndalama basi,chifukwa nthawi zambiri a peter amakonda poyankhula amakonda kukhamba za anthu mmalo moti atiuze za chitukuko cha dziko,Ine mmalo mwagulu la anthu ozuzula ndikungoti ,Mr mutharika musamaiwale kuti munasankhidwa ndi ife amalawi ,nde wa mkhulu sakwiya.

 3. Bwampini uja ndi wo ola mkamwa ndi chifukwa chake amalankhula zowola zokhazokha

 4. Iyeyo akunena kuti a malawi ndi akhalidwe lonunkha, iyeyo si m’malawi? Chitsiru cha anthu ndi iyeyo, munthu opanda khalidwe ameneyo. Watinyoza ife a malawi, chitsiru iwe kape weniweni, nyani, galu iwe chitsiru cha munthu. Usanyoze amalawi ngati wasowa chonena. Kulamula dziko kwakulephera wanva chitsiru iwe. Wandinyansa kwambiri.

 5. Akati pali Munthu Owola akuyenda nde Iyeyo Muntharika Chitsiru Cha chabechabe Iye Akamaziona Amazitenga kuti ndiye ndani

  Akagwere uko ndi kupanda maNO AKE MKAMWA galu ameneyo , Chimbatata ngati chimenecho a AMALAWI NANU MWAONA ZIMENE MUMAVOTERA PANO.

  GALU AMENEYO

 6. Iweyo ndiweso m’Malawi ndiye ukunena kuti a Malawi ali ndi khalidwe lowola nanga iweyo ndiwe ochokera dziko liti.
  Zikutanthawuza kuti Malawi ikulamuliridwa ndi mlendo. Nanga angaphunzitse a Malawiwo kusiya khalidweri ndindani?
  Tasonyezani utsogoleri otukula dziko. Inuyo ndi pang’ono zakumvazo, tafufuzani zomwe zikuchitika ku South Africa and Kenya. Kumathokoza kuti a Malawi ndife aulemu kwambiri.

 7. Koma anthu onunkhawo akuwadyelatu. Bwanji osangoyamika. Munthu uyu ndi onunkhaso mau ake.

  1. who heads those rotten peaple its him.That means we are all rotten may him be worse than us.

   By the way, its the very same rotten people who elected him . He is there becoz of there votes.And he is expecting the very pipo yo re elect him. To hhell with this hepocrecy.

Comments are closed.