Pofika 2019 sipakhala mseu wa fumbi – atelo Mutharika

5
Peter Mutharika

Peter Mutharika: Akuti misewu ya fumbi itha mdziko muno.

Ozapikisana ndi a Peter Mutharika mu chisankho cha 2019 azalimbe.

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika anena kuti iwo achita zodabwitsa ndi miseu ya dziko lino pofika mu chaka cha 2019.

Polankhuka pa msonkhano mu chigawo cha kumpoto kumene akukhalila pakali pano, a Mutharika ananena kuti Boma lawo layambapo kutukula dziko lino.

Iwo ananena kuti Boma lawo lili pakalikiliki okonza miseu ya dziko lino. Iwo ananena kuti chikonzelo chimene ayamba chokonza miseu chipitilila.

“Tikonza miseu yambili, ndipo tionetsetsa kuti pofika 2019 pasakhale mseu wa fumbi,”anatelo a Mutharika.

Iwo analonjeza kuti chitukuko ichi chipita Malawi yonse.

A Mutharika anatsimikizilanso anthu okhala mu chigawo cha kumpoto kuti Boma lawo litukula deralo.

Share.
  • Opinion