Siyani kuipitsira pa tchire, mangani zimbudzi, a Malawi alangizidwa

Advertisement
Malawi Toilet

Anthu mdziko la Malawi auzidwa kuti asiye chizolowezi chomazithandizira pa tchire ndipo alangizidwa kuti ayambe  kumanga komaso kugwiritsa ntchito zimbudzi zamakono moyenera.

Izi ndimalingana ndi mkhala pa mpando wa khonsolo ya boma la Chikwawa khansala Nankumba omwe anayankhula ndi nyuzipepala ino.

A Nankumba omwe anali mulendo olemekezeka, amayankhura izi loweruka pa Novembara 19 lomwe ndi tsiku lokumbukira zimbudzi pa dziko lose la pansi.

Elizabeth Kwelepeta
Kwelepeta: Anthu ayenera kusintha.

Mwambo wa chikumbutsowu kuno kwathu unachitikira pa bwaro la zamasewero la sukulu ya Dambe mdera la mfumu ya ikulu Maseya m’bomali ndipo unakumbukilidwa pa mutu wa dziko lonse oti ‘Chimbudzi ndi Ntchito’.

Mmawu ake khansala Nankumba anati anthu otsogola masiku ano anasiya kalekale chizolowezi chomaipitsira pa tchire ndipo anaonjezera kuti anthu amzeru amakhala ndizimbudzi ndipo amazigwirisa bwino mwanzeru.

Iwo anapitilira kunena kuti anthu asiye zikhulupiliro zomwe amakhala nazo zoti akamazithandizira mchimbudzi amaona ngati akuipitsira mnyumba yawo zomwe anati sizoona.

“Chimbudzi ndichofunika kwambiri pa moyo wa munthu chifukwa ndimalo omwe munthu umapeza mpumulo ndipo ife tikulimbikisa kuti banja lina lililonse likhale ndi chimbudzi chawo chawo ndicholinga chochepetsa matenda monga a kolera. Tsiku lalero pa 19 Novembara ndilofunikaso kwambiri mMalawi muno makamaka kwa anthu a m’boma lino la Chikwawa lomwe mothandizana ndi Nsanje chiwerengero cha anthu onyera pa tchire ndi chachikulu ndipo tili kalikiliki kufuna kuthetsa mtchitidwewu.” Anatero a Nankumba.

Mogwirizana ndi mkuluyu mkhala pa mpando wa bungwe la Water for People m’bomali lomwe linakoza ndikuendetsa mwambo onsewu, mai Elizabeth Kwelepeta anati kukhala ndichimbudzi kuthandiza kuchepetsa matenda monga kolera maka nyengo ino ya mvula.

Mai Kwelepeta anatiso ndiokondwa kuti pano anthu ambiri m’bomali ayamba kuvesetsa za ubwino okhala ndi zimbudzi ndipo anati iwo akulimbikisa izi mundondomeko yawo yotchedwa ‘Everyone Forever’.

Iwo anawonjezera kuti ndondomeko  ya Everyone Forever imalimbikisa kuti anthu mdziko muno azikhalala ndizinthu zawozawo monga zimbudzi komaso madzi aukhondo ndicholinga chokhala ndi a Malawi aukhondo komaso amphamvu.

Kafukufuku wa United Nations lomweso ndi bungwe lomwe linayambitsa mwambo okumbukira chimbudzi, waonetsa kuti anthu opitilira 2.4 million pa dziko lonse la pansi alibe zimbudzi ndipo amazithandizira a kutchire.

Advertisement

One Comment

  1. hahahaha koma Malawi!! Inu akhala bwanji ndzimbuzi ngat alindchimanga choti azidya? Alibe chakudya ndiye mukuganiza kuti nyonga zokumbira chimbuzi zichoka kuti? Zachizumbazumba izi

Comments are closed.