Ofesi ya za maphunziro m’boma la Mzimba ayidzudzula

Advertisement

Yemwe amayankhulapo pankhani zosiyanasiya zochitika m’dziko muno a Francis Liyati, adzuzura akulu akulu a zamaphunziro m’boma la Mzimba posalabadira ndi kuthana ndi nkhani za nkhanza zomwe m’phunzitsi wa mkulu pa sukulu ya Mzimba LEA Joseph Chirwa akuchitira aphunzitsi achizimai.

Chidzudzulochi chikudza pomwe pali nkhani yakuti m’phunzitsi wa mkuluyu akumawachitira nkhanza aphunzitsi akazi powakakamiza kuti akhale naye pa ubwenzi.

Poyankhula ndi Malawi24 kunyumba kwawo, m’modzi mwa aphunzitsiwa, Beatrice Longwe, watuluka poyera powulura kuti akuchitilidwa nkhanza pasukulupo ndi a Chirwa kamba kowakana ndipo iye wati  kangapo konse, wakhala akupita ndi khaniyi ku ofesi ya zamaphunziro m’bomali koma wakhala akukalipilidwa ndi akuluakulu akufesiyo omwe sawathandiza nkomwe.

“Ndakhala ndikudandawula nkhaniyi ku ofesi yathu ya za maphunziro kangapo konse koma nthawi zonse ndimangokalipilidwa ndi kuwophyezedwa kuti nkhaniyi ndingoyisiya”. Anatero a Beatrice.

Malingana ndi a Liyati, unduna wazamaphunziro uchitepo kanthu pa nkhaniyi mwachangu.

“Ndizosakhala bwino pamene dziko la Malawi tikulimbana ndikuthetsa nkhanza pakati pa a mai ndi a bambo pazipezekanso kuti anthu womwe amadziwa bwino za malamulo kumachitira nkhanza anzawo. Nkhani yomwe mphunzitsi wam’kulu pasukulu ya Mzimba akuganizilidwa kuti akuchita ndinkhani yosafunika, ndipemphe ofesi yowona kuti pasakhale kusiyana pakati pa amai ndi a bambo, komanso ofesi yowona chisamaliro cha wanthu ku nkhonsolo ya M’mbelwa komanso a Polisi kuti ifufuze zankhaniyi. Ndikuziwa kuti munthu afike ponena ndiyekuti watopa ndikhalidwe lotereli” atero a Liyati.

Malingana ndi a phunzitsi enanso atatu, a Chirwa anawafunsila ndipo atawakana, anawasamutsa pasukuluyo.

M’modzi mwa akuluakulu ku ofesi ya za maphunziro m’chigawo cha kumwera kwa boma la Mzimba, a Epmark Lwanja, atsimikiza kuti nkhaniyi akuyidziwa koma iwo sangayankhepo chilichonse chifukwa iwo siwololedwa kutero.

“Nditsimikize pano kuti ndizowona kuti nkhaniyo tikuyidziwa koma ndife womangika manja kuti tiyankhepo, ndikupempheni muyankhule ndi m’neneri wa unduna wazamphunziro”. Anatero Lwanja.

Wapampando wa ma bungwe womwe asali a boma ku m’bomalo, Christopher Melele, ati nawo akutsatira nkhaniyi mwachidwi ndipo kuti posachedwapa. atulutsa chikalata chawo ngati a mabungwe akamaliza kafukufuku wawo.

M’neneri wa Unduna wa Maphunziro, Mphatso Nkuonela, wati akudziwa bwino za nkhaniyo koma unduna uchita kafukufuku wakuya kuti upange chiganizo pa nkhaniyi.

Advertisement